Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kodi Maphunziro Osintha Malingaliro, Mtima Ndi Chuma Mthumba Amatanthauza Chani?

Maphunziro osintha malingaliro/ Mtima/ ndi chuma mthumba/ ndi a aliyense//ndipo amagwiritsa ntchito chikhulupiliro/ ndi Mau a Mulungu popeleka nzeru zolimbikitsa chitukuko pa moyo wa anthu pabanja/ komanso mudzi ndi dera lonse//

Mu maphunzirowa

  • Tiwunikilapo zolimbana/ komanso kuthetsa zikhulupiliro/ miyambo/ zizolowezi/ khalidwe kapena malingaliro oyipa/ omwe amalepheletsa chitukuko pogwiritsa ntchito mau a Mulungu//
  • Tikatelo/ tiwonapo mavuto osiyanasiyana/ omwe timakumana nawo ndi mmene tingathanilane nawo pogwilitsa ntchito zinthu zomwe ife eni tilinazo kale// Nzachiziwikile/ kuti mmene muthu amakhalira komamnso kuwonela zinthu zimatengera mmene iye akuganizira// Maganizo a munthu nthawi zambiri amagwirizana ndi zikhulupiliro za kwao komanso malo omwe munthu wakulira posatengela kuti zomwe akuganizazo nzoona kapena ayi//

Mau a Mulungu pa Miyabo 23 vs 7 amati “ Pakuti monga asinkha mkati mwache, ali wotere…”

Kenako…..

Tikawonapo za nsanamila zisanu za maphuzilowa

  1. KUZIDZIWA MWINI
  2. MASOMPHENYA
  3. CHIFUNDO
  4. MAUBALE ABWINO
  5. CHIKHULULUPIRIRO MU NTCHITO