Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Mau Otsogolera

Malawi ndi dziko la mtendere ndipo pamwamba pa zonse ndilodalitsika ndi zinthu ngati iz:

  1. Pa mahekitala 100 aliwonse/ mahekitala 20 ndi madzi a mitsinje kapena nyanja//
  2. Nthaka yolima iliponso kusiyna ndi maiko ena kumene kuli chipululu//

M’chaka cha 1978/ Malawi inali yopeza bwino kuyelekeza ndi China//

Nthawi imene Malawi imapeza ufulu uzilamulia/ inali yopeza bwino kuyelekeza ndi Taiwan//

Fuso mkumati kodi lero zili moterobe? Ngati sizilo choncho/ kodi nanda  n’chifukwa chiyani?

  • Kodi Mbeu zimafuna madzi kapena mvula/ ngati zimafuna madzi bwanji Malawi akukhala ndi njala chaka ndi chaka mitsinje ndi nthaka zochuluka zili mdziko muno?
  • Kodi Malawi ndi dziko losauka?/ Ngati lili losauka bwanji amwenye/ ma burundi ndi ena ambiri akuchita bwino m’dziko momwe muno?//
  • Kodi bwanji nanga ana akumanyetchela/ pamene dziko limalima chili chonse?

Alimi ambiri sapindula kapena kupita pa tsogolo ndi umili wawo/ngakhale ma business awo//ndipo kafukufuku akuonetsa kuti umphwawi obwela kamba ka kusowa kwa zakudya ukunka nakulibe// kodi izi zili chonchi chifukwa chani?// Pamwamba pa zonse a Malawi ndiwowopa Mulngu komanso opemphera/ koma bwanji mau a Mulungu pa Yohane 10-10b oti ndaza kukupansani moyo ochuluka sakukwanilisidwa kwa anthu ambiri?