Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Maphunzilowa Alunjika Pati

Maphunzirowa alimbikisa kuthesa malingaliro ngati awa:

  1. Sindingathe/
  2. Ndilibe kathu/
  3. Sindiziwa/
  4. Zabwino zonse zikhale zanga//

Zina mwa zikhulupiliro zomwe anthu a m’madera osiyanasiyana amakhulupilira

  1. Zikhululupirior za anthu opemphela
  1. Chikhulupiliro choti anthu ali ndi kuthekera (mzimu ndi chisankho) kosankha ndikuchitapo kathu/
  2. Chikhulupiliro choti anthu ndi adindo adziko ndi zonse ziri mmenemo
  3. Chikhulupiliro choti zinthu ziribe malire ndizomwe zimapezeka mu nthaka
  4. Chikhulupiliro choti ali ndi kuthekera koganiza ndikuchita
  5. Chikhulupiliro choti ali woyankha kwa Mulungu muzochita zawo
  6. Chikhulupiliro cha chisomo, kukonda ndi kukhululuka
  7. Chikhulupiliro choti aliyense atha kupeza bwino
  8. Chikhulupiliro choti munthu ndi thupi ndi mzimu
  9. Chikhulupiliro cha pa malamulo owumba munthu

B. Zikhulupiliro za anthu osakhulipilira kuti kuli Mulungu

  1. Kukhulupilira kuti anthu amatsogozedwa ndi mphamvu za chibadidwe
  2. Kukhulupilira kuti anthu ndi zinyama zopezeka mwa Mwayi
  3. Kukhulupilira kuti palibe phindu kapena cholinga cha moyo
  4. Chikhulupiliro choti zinthu sizingapezeke modutsa pomwe tikuganizira
  5. Chikhulupiliro choti munthu ndi thupi
  6. Chikhulupiliro choti Palibe cholondola komanso cholakwika, koma kuti aliyense ndi lamulo payekha
  7. Chikhulupiliro choti zofuna zonse ndi maganizo zidzivomerezedwa
  8. Chikhulupiliro choti “idyani, imwani poti mwina mawa kulibeko
  9. Chikhulupiliro choti matenda ndi kudwala ziribe kulumikizana ndi mzimu

C. Malingaliro oti munthu ali ngati zinyama (Za mizimu/anthu osakhulupilira Mulungu/chi hindu)

  1. Chikhulupiliro choti anthu ndi chilengedwe zimalamuliridwa ndi mizimu komanso mphamvu zosawoneka
  2. Chikhulupiliro choti munthu ndi mzimu womangidwa mu thupi
  3. Chikhulupiliro choti kapezedwe kamunthu kagonera mmachitidwe ake akale
  4. Chikhulupiliro cha ziwanda
  5. Chikhulupiliro choti sitingasinthe mtsogolo chifukwa cha kale lathu
  6. Chikhulupiliro choti kudwala ndi matenda zimadza chifukwa cha mizimu
  7. Chikhulupiliro choti mbiri ya kale imangobwerezedwa
  8. Chikhulupiliro choti chowona ndi choipa chimachitika malinga nkufuna kwa mizimu
  9. Chikhulupiliro choti amuna ndi apamwamba koposa akazi