Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Theme IV. Maubale

Kwa mphindi zisanu anthu agawidwe magulu awili ndikupanga masewelo opanga nzele wautali pogwilisa zimene ali nazo

Anthu agawidwe magulu awili. Chiwelengero cha azibambo ndi azimayi chikhale chofanana mmaguluwa

 “Gulu lililonse likhale ndi phindi zisanu zopangila nzere wautali pogwilisa zimene ali nazo.

Konzani Pulani ya gulu lanu

Aphunzitsa akati “yambani” kambilanani ndi kukonza pulani ya gulu lanu imene ingakuthandizeni kupanga nzere otalikitsitsa. Yesetsani kuti gulu lanu lipeze njira yoti litha kupangila nzere otalikitsitsa kuposa anzanu onse!

Mukhonza kuona kuti sewelo limeneli/ likutionetsela kufunika kogwilira ntchito limodzi, kugwilitsa ntchito katundu yemwe aliyense wa ife ali naye kupititsatsa chitukuko patsogolo. Kutsogoloku tizaunikaponso zomwe taphunzira mu phunzilori polumikizana ndi maphunziro ena.

Debrief Session (kukambilana za M,buyo)

Kodi gulu linapanga mzere wautali linakwanisa bwanji?

Kugwilira ntchito limodzi pomvelana komanso kulolena/ Kukhazikisa ndondomeko zabwino ndikuzisatila//Kuganiza  mozama m’kachitidwe ka zinthu/Chikhuulupiriro ndikudekha ndinso Kupilira//

Kodi kutalika kwa mzere mwafikilaku ndiye anali mathelo anu? Kapena munakatha kuonjezerapo?Chinakuimitsani ndi chani?

- Kodi munayima mutawona kale kuti mwawaposa anzanu? Kodi mmadela mwathumu tikukanika kuchita  moposela chifukwa tikuona kuti tawaposa ena?

-Kapena mwina pali zinthu zina timazidelera chifukwa zimaoneka kuti ndizopanda ntchito monga zingwe za nsapapto popanga mzere

-Kapena mwina anthu ena amakhala aliuma popeleka zinthu zawo kuti zigwilisidwe ntchito

Fufuzani pa banja panu kapena kudela kwanu kuti ndi chiyani chikupangisa kuti anthu asapite patali.

Kodi agulu linalo chinawakanikisa kupanga mzere oposa anzawo ndi chiyani?

Ndi udindo wa mtsogoleri kusegula maso ndikuunikila anthu kuti akaone ndikugwilitsa ntchito zinthu zimene ali nazo komanso kugwira ntchito limodzi ngati gulu kuti akhale ndi tsogolo labwino

Welengani  Yohane 4:1-42 ndipo mukambilane kuti nkhani ya ubale wabwino ikuphunizitsidwa bwanji

Mbiri pang’ono yamawu awelengedwawa

Chiyambi cha kusiyana kwa a Izilaeli  ndi a Samaria

Fuko la Izilayeli linagawikana pawili nthawi ya ufumu wa Rehoboamu (1Mafumu 12). Izilayeli  anali ndi mitundu khumi ndipo amakhala ku mmawa ndipo Yuda ndi Benjamin anakakhala pawokha. Ndipo nthawi yomweyo magulu awili amenewa anayamba kusamakhalisana bwino ndi kumwelana madzi

Mmene a Yuda amawaonela azimayi

Kutengela mbiri ndi chikhalidwe cha Ayuda, mamuna samayenela kulankhula ndi mkazi pagulu makamakanso mphunzitsi wa Mau a Mulungu. Azimayi samaphunzitsidwa chilamulo pa gulu. Mzimayi kwake kunali kumvera basi

 

 

Yankho la Yesu

  •  Mzimayi anabwera pa chitsime kudzapeza madzi ngati chosowa chake cha moyo koma Yesu akumpasa chosowa cheni cheni chokondedwa ndi kuvomelezedwa ndi anthu
  •  
  • Yesu akuziulula yekha kuti ndi Mpulumutsi ndipo kuti anabwela kuzayanjanitsa anthu onse ndi Mulungu. Mzimayi uja akubwezeletsedwa komanso akuyanjanitsidwa ndi Mulungu

 

  • Yesu akuoneTsela utsogoleri wabwino poyanjanitsa ndikubwelesa maubale posayanganila mtundu kapena malire. Monga iye okhala muyuda sakanayenela kulankhulana ndi msamaliya komanso mzimayi

Mkumano ndi mmayiyu ukupulumusa muzi onse (vs 39- 42)