Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Cholinga Cha Maphunzirowa

Maphunzirowa akonzedwa  kuthandiza anthu kuzindikula luntha/ kuthekela/ katundu/ komanso zinthu zimene ali nazo ndikuyamba kuzigwiliza ntchito kuti sinthe miyoyo yawo/ ndi anthu ena kuti ayambe kukhala moyo umene Mulungu anakonzela ana ake// Munthu aliyense ndiye akuyenela kuzifunsa mafunso awa:

  1. Ndine ndani?
  2. Ndinachokela  kuti?
  3. Cholinga cha mulungu pondilenga ndi chiyani?
  4. Ndili ndikuthekela kwanji? Nanga ndili ndi maluso anji?
  5. Kodi ndikupitas kuti? Nanga pano ndili pati?
  6. Ndili pano chifukwa chiyani?
  7. Ndingatani kuti ndikwanilise cholinga kapena masomphenya anga?