Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Theme III. Chifundo

Welengani ndi kukambilana Luka 8:40-56

PHUNZIRO

Pamene Yesu anaima ndikulankhula naye mayi okha mwazi uja zinaonetsela chifundo chimene chinachotsa chitonzo chokanidwa pakati pa anthu ndikuziyanganila pansi. Ndizofunika kuonetsa chifundo kwa anthu ovutia, aumphawi komanso okanidwa mudela mwathu

Anthu akambilane njila zimene angawathandizile anthu ovutika mosiyanasiyana mudela la kwawo

Zinthu zimene zimaonesela chifundo

  • Chikondi pa Mulungu
  • Kukonda kugwila ntchito zothandiza ndikutukula ena
  • Kuthandiza osauka
  • Kukhala odekha ndiwachidwi
  • Kulimba mtima poyamba zinthu za tsopano

Mulungu amachitila chifundo aliyense Okhululupilira ali ndi udindo obwezeletsa zinthu zoonongeka// Chifundo ndiye gwelo lokonda kugwila ntchito ndi anthu osowa// Mulungu anatidalitsa ife ndi zinthu zosiyanasiyana / kuti tikhale m’dalitso kwa ena//

 Mtima wa chifundo umapangitsa ena kumva kuvomelezedwa komanso kuwelengedwa ngati anthu ofunikilanso// Munthu akamapasidwa mpata omveledwa posatengela mmene amaonekela/ iye amasimikizika kuti sali yekha//Mtima wa chifundo umaonekela poyimila anthu pa chilungamo / komanso kuonesetsa kuti palibe kusankhana pakati pa anthu/ /Mtima wa chifundo umathandizila kuziwa zosowa za ena mwa msanga ndikuchitapo kathu//Mtima wa chifundo umatipangisa kuti tokhonza kuyimika ma plani anthu kuti tithandize ena kaye//

Pakuti mapiri adzachoka ndi zitunda zidzasunthika; Koma kukoma mtima Kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano change cha mtendere, atero Yehoha amene wakuchitira iwe chifundo” Isaiah 54:10