Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Theme V. Chikhulipiliro mu Ntchito

Ichi ndi chionesero/ kapena umboni wa kusinthika kumene kwachitika pamene munthu asiya mchitidwe wakale/ ndikuyamba cha tsopano ngati mabizinesi/ kulima posatila njila zamakono/ kuyanjana ndi a banja kapena ndi midzi/  komanso kuyamba kusonkhanitsa anthu pamodzi chifukwa cha chitukuko//

Kwa mphindi zisanu gulu lipange sewero lowoloka mtsinje

  • Jambulani chitsanzo cha mtsinje pansi ndipo muikemo zizindikilo za powolokera monga miyala mmene afotokozera mmusimu.
  • Phunzitsani anthu atatu za momwe phunzilori liyenera kuchitikira ndipo iwowo akachita bwino aonetse ku gulu lonse mmene zikuyenera kukhalira.
  • Akatha kuchita phunzilori  kambilanani za izi;.
  • Chimachitika ndi chiyani musewero?
  • Kodi anthuwa aliyense payekha amayimila gawo lanji la anthu mmudzi?
  • Kodi mbali ziwiri za mtsinje zikuyimilira chiyani mmadela mwathumu?
  • Nanga minyala ija ikuyimilira chiyani?
  • Kodi ndi njila ziti zimene zinagwilitsidwa poolosa anthu aja?
  • Kodi njila iti imene anthu amayikonda? Nanga yabwino ndi iti?
 

Zoyenera kuchita msewelo lowoloka mtsinje

Jambulani mizere iwiri yotalikana bwino kuimila matsidya awiri a mtsinje wauukulu ndithu.  Ngati pali pa simenti gwiritsani ntchito zingwe.

Ikani mkati mwa mtsinjewu pa pepala kuimilira miyala yowolokelapo komanso pepala lokulirapo pakati kuiimilira ka chilumba.

Anthu awiri afike pa mtsinjepo kufuna kuoloka koma madzi akuthamanga kwambiri ndipo iwo akuchita mantha kuoloka

Munthu wina wachitatu afika pamalopo ndipo waona mavuto a anthu awiriwa.  Akuwathandiza kuti awoloke powaonetsa moti aponde koma anthuwa akuopabe kenako wadzipereka kuti amubereke mmodzi mwa anthu awiriwa.

Pofika pakati pa mtsinje watopa ndipo wamutsitsa anamubereka ku msana uja pa ka chilumba kaja.

 

Ngakhale watopa wabwerera kumatenga wina anatsalira uja. Poti watopa sangamubelekenso koma wamugwira pa mkono ndipo pang’ono pang’ono ayamba kuoloka poponda miyala yowolokera

Atafika pakati othandizidwa uja mantha ayamba kuchepa ndipo wayamba kuwoloka molimba mtima payenkha mpaka kukwanitsa kupita tsidya lina.

Atafika tsidya lina onse ndi okondwa kwambiri ndipo waphunzitsidwa kuolokayu abwereranso kukamuthandiza mzake anatsala pa kachilumba uja kuti aoloke

 

 

 

Tingagwire bwanji ntchito limodzi/ kuti tithandizane ndi anthu a ku mudzi kuti akhale odzidalira ndi okhazikika/ pamene akuthana ndi zovuta zosiyanasiyana zomwe amakumana nazo// Utsogoleri ndi ofunika kwambiri pothandiza mudzi kuti ukhale odzidalira okha/ komanso kupewa kudalira kuthandizidwa//

Kuwelengera Ndalama zolowetsa ndi cholinga choti munthu upange phindu komanso Ukadaulo otha kuchita zokambilana  – Luka 14:28-30

28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza? 29 Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, 30 ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.

  • Kodi tikuphunzirapo chiyani mu nkhaniyi za kupanga ma pulani?
  • Yesu anabadwila mbanja la bizinesi ya ukalipentala ndiye amaziwa kufunika kwakuwelengela bwino bizinesi kapena ntchito isanayambe?
  • Kodi kupanga ma pulani mosamala kumatiteteza bwanji pamene takula mu chikhulupiliro chathu chokakwanilitsa zinthu zazikulu?

Mtima osaopa pa bizinesi

Mathew 14:22-23

22 Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke. 23 Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha

Mathew 13:44-46

44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwache achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu. 45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: 46 ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo

  • Kodi mundime zimenezi tikuphunzira chiyani za kusaopa popanga bizinesi?
  • Kodi chinthu cha mtengo wapatali kwambiri kwa inu ndi chani? Mukuyenera kupanga chani kuti muchipeze komanso kuti muchiteteze chikapezeka?
  • Kodi mudzi wathu ungagwire bwanji ntchito pamodzi kuti ukathe kuzindikila chinthu chomwe chili cha mtengo wapatali kwambiri pakatipathu ngati mudzi?

KUUNIKILA MABIZINESI

Ulimi wa Galiki (Adyo)

  • •1 ekala ya Galiki = 7tonnes (7,000kg)
  • •1kilo galiki amagulitsidwa pa  MK5, 000
  • • 30,000kgs = MK35, 000,000.00
  • •Galiki amacha pakutha pa miyezi 5 yokha basi
  • (MK10,000/kg = MK70,000,000.00)
  • (MK20,000/kg Msika wa ku Ameleka = MK140,000,000.00)

Ulimi wa Tomato

  • •1 ekala ya Tomato pamakhala  mbewu 10,000  (nthawi zina zimatha kufika  30,000)
  • •Mtengo umodzi wa Tomato umabereka tomato 40
  • •Tomato mmodzi amagulitsidwa pa MK50
  • •Chonco pa 1 ekala ya Tomato munthu atha kupeza MK20, 000,000.00
  • •Tomato amacha pakati pa miyezi 3 mpaka 5

Ulimi wa anyezi

  • • 1 ekala ya anyezi = mbeu 120,000
  • •Mbeu imodzi ya anyezi imabereka anyei mmodzi
  • •Anyezi mmodzi amagulitsidwa pa  MK50
  • •Choncho 1 ekala ya anyezi  munthu atha kupeza MK6,000,000.00

 

Zoyenela kuganizila

 

  1. Kodi alimi anthu amakolola kapena kupeza ndalama mmene zilili mmwambamu?
  2. Ngati sizili choncho, ndi chifukwa chiyani?

-Amadzala mbeu zochepa pa ekala kuyelekeza ndi mmene zingafunikile chifukwa chosatsata ndondomeko zakazalidwe

-Amakolola zochepa kuyelekeza ndi zimene zikuyenela chifukwa chosatsata ndondomeko ya kalimidwe

-Amagulitsa mitengo yosika chifukwa amalima mbeu zili mpweche?

        3   Alimi angatani kuti azipeza zotere?

Kusatila ndondomeko za malimidwe amakono/ Kupanganso ulimi wanthilira kuti azilima mbeu zimene zikusowa/ Kugulitsa mmagulu/ Kulima mbeu zosiyanasiyana/ kusungako ziweto komanso kuzala mbeu pa ekala nthawi zosiyana kuti zisazache nthawi imodzi//

UTHENGA OYENELA KUUKUMBUKILA NDIKUGWILISA NTCHITO

  1. Cholinga cha mulungu pomulenga munthu chinali choti akhale ndi moyo wabwino/ wanthazi/ osasowa kathu komanso wa mtendere//  (Gen 2)
  2. Mulungu anamulenga munthu kuti agwire ntchito ndikusamalira chilengedwe (Gen2 vesi 15). Zoti ntchito inapelekerdwa munthu atachimwa (Gen 3) ndi bodza lamukukhuniza/
  3. Mulungu amafuna mabanja azikhala mwa mtendere//
  4. Imfa ya yesu inatiombola ku chilango ndi uchimo