Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Theme II. Masomphenya

Mphunzitsi ayambe mutu umenewu powafunsa anthu kuti apachike misomali 17 pa msomali umodzi. Awapase thabwa, loboola pangono pakati ndi misomali 17

“Gulu lanu lipachike misomali 16 pa nsomali umodzi.

Yesesetsani kuchita izi mwachangu, ncholinga choti mukhale gulu loyamba kupeza yanko//

 

Phunziro mu chochitika chimenechi

  1. Masomphenya amaoneka ovuta kapena osatheka akamayamba
  2. Masomphenya amafunika kupilira/ kudekha/ chikhululupiriro/ nzeru komanso kulimbika kuti akwanilisidwe
  3. Masomphenya amafunika mgwilizano ndi kumvelana
  4. Masomphenya amafunika kugonjesa zotchinga
  5. Kathu kena kalikonso komwe munthu ali nako katha kugwilitsidwa ntchito mwanzeru kukakwanilitsa chomwe munthu angafune kukwanilitsa

Miyambo 29:18

“Popanda Vumbulutsa anthu amasauka; Koma wosunga chilamulo adalitsika”

Ndikofunika zedi kuti munthu aliyense akhale ndi masomphenya otsatilika bwino ndipo akhazikitse njila zokwanilitsila masomphenyawo