Module Articles

Mpunga

Mpunga

Kusankha Malo

  • Sankhani munda umene sunabzalidwepo mpunga mu mchaka chapita wa dothi losunga madzi komanso lopanda chonde kwambiri. Malo akhale ndi madzi okwanira othililira

Kusosa

  • Gwiritsani ntchito chotchetchera, chikwanje, khasu ndi leki pososa mmunda. Komanso otchani zotsala mmunda.

Kugaula

  • Gaulani mozama kuti muphe udzu kapena poudula ndikuonetsa mizu pamwamba kuti iwume, m’pweya uzidutsa bwino munthaka komanso kusunga madzi potengera mtundu wa dothi. Salazani munda kuti ukhale osatsetsereka. Kuthandiza kuti madzi azisungika ndi kuthandiza kuti mpunga uziokereka bwino.