Mpunga umalimidwa kwambiri ndi alimi ango’ang’ono mdziko muno. Mbewuyi imalimidwa motsatira chimanga, m’mbali mwanyanja, ku Phalombe, ku Chigwa cha Shire ndi ku Nyanja ya Chirwa ngati mbewu yoyamba. Mbewuyi imalimidwa mmasikimu pothilira, mzidikha kapena kumtunda podalira mvula. Mpunga umadyedwa kapena kugulitsidwa.
Pomaliza pa phunziroli mlimi ayenera kudziwa izi:
FAYA (14M69)- Onunkhira, umafufuma ndiponso umatenga masiku 150 kuti uche
BULU-BONETI – Okoma komanso onunkhira, umalimidwa mu nyengo zonse. Umatenga masiku okwana 120 mpaka 130 kuti uche, komanso zokolola zimachuluka
SENGA (IET 4094)- Olimidwa nthawi ya mthilira. Umatenga masiku okwana 116 kuti uche
CHANGU (IRI 1561- 250- 22)- Umalimidwa nthawi ya mthilira. Umatenga masiku okwana 119 mu nyengo ya mvula ndi masiku okwana 155 mu nyengo ya mthilira.
NUNKILE (PUSA 33)- Umalimidwa nthawi ya mthilira. Utha kulimidwa kawiri pachaka chifukwa choti umatenga masiku 112 mu nthawi ya mvula komaso masiku 140 mu nthawi ya mwavu kuti uche
Alimi ena amagwiritsa ntchito mbewu zina zakale monga Kilombero, Singano, Kalulu ndi Mwasungo. Alimi ayenela kulimbikitsidwa kuti azigwiritsa ntchito njira zovomelezeka za ulimi kuti azikolola zochuluka.