Tizirombo todziwika tomwe timaononga mpunga ndi monga; bwamnoni, mphuzi, nsabwe za mizu, agulugufe, (rice skipper), bololo, chiswe ndi ntchemberezandonda.Tetezani mpunga popalira mwakathithi kapena kupopela mankhwala omwe amapha tizilombo monga cabaryl, cypermethrin, kapena fenitrothion.
6.2Matenda
- Chiwawu chobwera mochedwa - chimayambika ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa Fungus. Zizindikiro zamatendawa zimaoneka nthawi imene mpunga wayamba nthambi. Matendawa amachepetsa zokolola. Bzalani mbewu zomwe zopilira kumatendawa. Popelani mankhwala a mancozeb ndi carbendazim pamene mpunga wagwidwa ndi matendawa.
- Chiwawu chobwera moyambilira - chimayambika ndi kachirombo kosaoneka ndi maso kotchedwa bacteria ndipo chimagwira mbande zampunga. Masamba ogwidwa ndi matendawa amakhala otuwa, obiliwira ndipo amakhwinyata. Matendawa akapitilira, masamba amakhala a chikasu zotsatira zake mpunga umauma ndikufa. Thirani feteleza wa nitrogen kuti matendawa achepe.
- Nthomba zachikasu (Rice Blast)- Matendawa amayamba ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa fungus. Matendawa amapezeka kwambiri ku Nkhata Bay. Masamba amaoneka ndi zipsela-zipsela zomwe zimaoneka zosiyana potengerana ndi mtundu wa mpunga
- Bzalani mbewu zopilira ku matendawa.
- Kuwola kwa makoko (Sheath rot) – Matendawa amayamba ndi kachirombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus. Mpunga ndi mankhusu zimawola. Bzalani mbewu zopilira kumatendawa. Popelani mankhwala a mancozeb ndi benomyl kuti muphe tizilombo mu dothi tomwe timayambitsa matendawa.
- Matenda amene amabweretsa nthomba zachikasu (Rice Yellow Mottle Virus) Matendawa amayamba ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus. Mpunga siukula bwino ndipo umakhala ndi nthambi zochepa, umakhala ndi mabala, masamba achikasu komanso opunduka ndipo mbewu imafa. Bzalani mbewu zopilira ku matendawa.