Chimanga
Ulimi Wa Nsomba
Kusankha Malo
- Kulima kumayenera kuyamba mwansanga mvula ikatha kapena mukangomaliza kukolola.
- Munda umayenera kutipulidwa mozama pa mlingo okwana 30cm kuti uthandizile kuwolerana kwa manyowa komanso kalowedwe ka mpweya wa bwino mu dothi.
- Mizere italikirane 75cm kapena 90cm
- Sosani mmunda pogwiritsira ntchito makasu, zisikilo ndi zikwanje.
- Gwiritsani ntchito mankhwala a Round Up pakupha njere.
Chiwerengero cha mbewu
- Kuchuluka kwa mbewu kumatengera katalikidwe ka mizere, kuchuluka kwa mapando komanso mtundu wa mbewu yomwe yabzalidwa. Kunavomerezedwa kugwilitsa ntchito ndondomeko ili musiyi podziwa kachulukidwe ka mbewu
- Njira ya makono yomwe imakhala ndi mizere yotalika 75cm ndi kutalikirana kwa ma phando 25 cm kumatipatsa chiwerengero cha mbewu zochuluka 53,333 pa hekitala
- Pogwiritsa ntchito njira yachikale yomwe imakhala ndi mizere yotalika 90cm mapando otalikilana 90cm kumatipatsa chiwerengero cha mbewu zochuluka 37,037 pa hekitala