Chimanga
Ulimi Wa Nsomba
Kubzala
- Bzalani ndi mvula yoyamba yobzalira ikagwa. Mizere italikirane 75cm kapena 90cm
- Palilani udzu ukangomera kapena gwiritsani ntchito mankhwala opha udzu.
- Bandilani ngati mwapanga miziere
- Pakizani mapando amene mbewu siinamere.
Kuthila feteleza
- Thilani feteleza okulitsa wa 23:21:0+4S tsiku lomwe mukubzala moyenera pogwiritsa ntchito zitsekelero za fanta kapena kokakola pothila feteleza paphando lili lonse.
- Thilani Fetereza wa chiwiri wa UREA pakatha masiku 21chimanga chikamera.