Kapuchi – Tizilomboti timaboola mapesi ndi kudya makoko a chimanga ndipo zimachepetsa zokolola. Bzalani moyambilira kuti mupewe tizilomboti. Popelani mankhwala a Cypermethrin.
Ntchemberezandonda – zimadya masamba a chimanga ndipo zimachepetsa zokolola. Poperani mankhwala a Cypermethrin.
Nankafumbwe – amadya zokolola. Thilani mankhwala a Actellic.
Chiswe – chimagwetsa mapesi komanso chimadya chimanga chomwe chagwa. Bandilani mofulumira.
Makoswe – amadya chimanga chokhwima kumunda ngakhale mmalo osungira. Ikani ma Rat Guard komanso nkhokwe zovomerezeka
Matenda a Chimanga;
Kontho – Amagwira chimanga chomwe chayamba kubeleka. Bzalani mbewu yopilira ku matendwa
Chiwawu – Chimagwira masamba a chimanga ndipo masambawo amakwinyika. Bzalani mbewu yopirira ku matendawa. Popeplani Mankhala a Cypermethrin
Kuwola kwa Mizu- Matendawa amapezeka kwambiri ku malo omwe kuli dothi la lowe. Bzalani mbewu zopilira kapena popelani Makhwala a Cypermethrin.
Kuola kwa mapesi- matendawa amapangitsa kuti chimanga chithyoke, bzalani mbewu zopilira kumatendawa.