Mpunga
Kasamlidwe ka mbeu
Kuthirira mpunga
- Mpunga umafuna madzi ochepa masiku 8 mpaka 10 mutangookela. Onjezelani madzi pamene mpunga ukukula mpaka kufikila nthawi imene mpunga wacha. Palirani mowilikiza pamene udzu wamera, Kuchepetsa udzu makamaka mmasiku 15 mpaka 20 oyambirira mutangookera zimathandiza kuti mpunga ukule bwino.
Kuthira feteleza
- Thirani Feteleza okulitsa wa 23:21:0+4S mophatikiza ndi 10Kg feteleza wa S/A pa hekitala pa nthawi yookela kapena thirani feteleza pakatha ma wiki atatu pamene mpunga wamela mmunda. Thirani feteleza wa UREA pakatha masiku 30 kapena 40 mukangobzala kuti nthambi zichuluke.