Module Articles

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Kusinthika Mmalingalilo, Mtima Ndi Mthumba

Theme I. Kuzizindikila

Genesis 1 verse 26-28

26 Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”

27 Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu;

analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

28 Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse.

TANTHAUZO LA MAU AMENEWA

  • Anthu onse analengedwa mu chifanizo ndi chikhalidwe cha mulungu kuti akhale ogwira olenga nawonso, kugwila ntchito ndikupindula ndi ntchito ya manja awo
  • Munthu aliyense (mamuna kapena mkazi anadalisidwa ndikupasidwa ulamuliro pa zolengedwa
  • Kugwila ntchito ndiye udindo wa munthu (Gen 2 verse 15) Ulesi ndi kuzitembelera
  • Uchimo ndiye gweru la umphawi ndipo kugwa kwa munthu. (Gen 3 ) chiyambi cha kutaya moyo wabwino umene mulungu anaupeleka kwa munthu
  • Munthu atagwa (Gen 3) sanatembeledwe koma njoka ndi nthaka
  • Themberero la nthaka linachosedwa (Genesis 8 verse 22)
  • Ngakhale munthu anagwaa koma wanjanisidwa ndi mulungu kudzela mwa yesu mkhrisitu (2 Corinth 5vs 17-18, Eph 2 vs16, Col 1 vs 20-21)
  • Chikhalidwe chili chonse chili ndi miyambo ya bwino  ndiyoyipa, choncho ndibwino kumvesesa mmene miyambo ndichikhalidwe zingapangisile moyo kupita patsogolo kapena kubwelera mmbuyo

Mulungu Yekha ndi amene angathe kumasula anthu kunsinga za umphawi ndi mantha ku ufiti and zikhulupiriro pa za nyanga