Module Articles

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

KUSAMALA SOYA

Soya ndi imodzi mwa mbewu zofunikira kwambiri m’Malawi muno. Soya ali ndi michere yomanga thupi (36%), michere yopatsa mphamvu (30%) komanso michere ina yofunika nthupi ndi mitsitsi yothandizila kugaya zakudya mu thupi la munthu. Chifukwa cha ichi, soya ali oyenera kukhala gawo la zakudya zomupatsa mwana pamene akusiya kuyamwa makamaka m’madela odalila chimanga. Soya ali ndi mafuta ochuluka (20%) omwe amatha kuwengedwa.

Ulimi wa soya ndi njira imodzi yomwe allimi makamaka achizimayi amapezelapo ndalama. Ku Malawi soya ali ndi msika opezekeratu chifukwa cha kufunika kwake kumene mabungwe omwe si aboma akulimbikitsa komanso chifukwa cha mafakitale omwe akumakonza soya kukhala zakudya zosiyanasiyana ngati nyama ya soya.

Ufa wa soya osakaniza ndi chimanga ndiwopatsa thanzi ndipo umagwiritsidwa ntchito kwambiri ngati chakudya cha ana chifukwa muli michere yambiri yomanga thupi.

Ufa wa soya osakaniza ndi chimanga

ZOFUNIKIRA  KOMANSO NDONDOMEKO

Zofunikira

  • Soya
  • Chimanga
  • Moto
  • Chigayo
  • Zipangizo zolongedzera
  • Makina omatira

Ndondomeko yopangira ufa wa soya osakaniza ndi chimanga

1:  Petani ndi kusankha chimanga chanu ndi soya wanu kuti muchotse miyala ndi zinyalala zina. Kusankha kumathandiza kuti chakudya chathu chikhale chabwino, chosapeleka chiopsezo pa moyo wa munthu, komanso chovomerezeka.  .

2: Kazingani soya wanu mpaka atapsa bwino (at 1000C for 20 minutes). Kukazinga soya kumapangitsa kuti ufa uzakhale onunkhira bwino, uzagaike mosavuta komanso kukazinga kumachotsa ma poyizoni ena omwe amapangitsa kuti michere yomanga thupi isapezeke mokwanira mu ufawu.  Soya atha kukazingidwa pa chiwaya kapena mu uvuni ophikira mpaka atapsa bwino

3:-Sakanizani kapu imodzi ya soya okazinga ndi makapu anayi a chimanga (kapena kuti kilo imodzi ya soya okazinga ndi ma kilo anayi a chimanga).

Soya

4: Gayani chimanga ndi soya zomwe zasakanizidwa

Chigayo cha soya

5: Longedzani mumapaketi aukhondo ndipo matani

        

Ufa wa soya wa m’paketi

 

 

Ndondiomko yopangira ufa wa soya ndi chimanga