Jinja ndi chomera chomwe chakhala chikugwiritsidwa ntchito ngati mankhwala kwa nthawi yaitali pa dziko lonse. Jinja amagwiritsidwa ntchito pochiza matenda osiyanasiyana monga nyamakazi, kubinya, nsungu za pakhosi, kupweteka kwa minyewa, kudzimbidwa, kusanza, kuthamanga kwa magazi, kutentha kwa thupi, kuiwalaiwala ndi matenda ena opatsirana. Jinja ali ndi kuthekera kosokoneza tizilombo ta mtundu wa bacteria pachifukwa chimenechi, jinja amagwiritsidwa ntchito ngati makhwla a nthenda zoyambitsidwa ndi tizilombo ta mtundu wa bacteria wu. Ufa wa jinja umapangidwa kuchokera ku jinja yemwe wakhwima bwino (wakhala miyezi isanu ndi inayi kuchokera pa tsiku lodzala). Jinja owuma ndi wotchuka kwambiri ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mankhwala komanso nati zonunkhiritsa chakudya.
ZOFUNIKA KOMANSO NDONDOMEKO YA KAPANGIDWE
zofunika
ndondomeko ya kapangidwe ka ufa wa jinja
1: tsukani jinja ndi madzi aukhondo mukangomukolola kuti madothi onse achoke komanso kuti jinja wanu akhale owala. Jinja atha kutsikidwa ndi madzi a pampopi, mundowa, kapenaso kugwiritsa ntchito makina otsukira. Kutsuka kumathandiza kuti ufa wajinja wathu ukhale wa pamwamba komanso wosapereka chiopsezo kwa anthu omudya. Jinja wamuwisi asasiyidwe pa mulu kwanthawi yaitali chifukwa amayamba kuonongeka.
Makina otsukira zinthu monga jinja ndi mbatata
2: Dulani jinja wanu mu tizidutswa toti tikhoza kuyanikidwa. Kudula kukhoza kutheka ndi mpeni komanso makina odulira jinja. Kudula jinja kumathandiza kuti awume msanga akayanikidwa.
Makina odulira jinja
Step 3: umitsani jinja pomuyanika pa dzuwa, kugwilitsa ntchito makina a dzuwa kapena makina oyanikila a magetsi kuti awume msanga komanso asalowe fumbi. Jinja owuma bwino asadutse mlingo wa madzi wa 7 to 12% ndipo amapepuka kwambiri kuyelekeza ndi wamuwisi.
Makina oumitsira jinja
4: Gayani jinja wanu mu chigayo.
Jinja, ufa wa jinja, komanso chigayo cha jinja
5: longedzani jinja wanu mu makontena aukhondo. Cholinga cholongedzela ndikuonetsetsa kuti ufa wa jinja uli otetezedwa ku zinthu zosiyana siyana mzomwe zingathe kuononga. Kupatula apo, kulongedza ndikofunika chifukwa kumathandiza kufalitsa mauthenga aza mkatimo.
ufa wa jinja
Nndondomeko kakonzedwe ka ufa wa jinja