Module Articles

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

ZOYENERA PA UKHONDO PA MALO OPANGIRA CHAKUDYA

Kutsuka komanso kuthita mankhwala

Popewa kuwonongeka kwa chakudya, ziwiya ndi zipangizo zonse zikuyenera kutsukidwa kawirikawiri. Zinthu ziyenera kuthiridwa mankhwala ngati pali pofunika kutero. Malo kapena chimene chimakhudzana ndi chakudya chonyowa ziyenera kutsukidwa zikangotha kugwilitsidwa ntchito. Malo kapena chida chomwe chimakhudzana ndi chakudya chowuma zitsukidwe moyenera molingana ndi ukadaulo wa malowo kapena chidacho.  Ngati kuli kofunikira zipangizozi zimasulidwe kuti zitsukidwe moyenera.

Pewani kugwilitsa ntchito zipangizo zopukutira za chitsulo potsukira zipangizo ndi ziwiya zopangira chakudya kuwopetsa kuti zingaononge chakudyacho. Zipangizo ndi ma payipi ena ndizofunika kutsukulizidwa ndi madzi zisanagwilitsidwe ntchito. Nthawi zina madzi otsukuzilawo ayenera kukhala ofuna mosapitilira ma digili 45. 

Zimbudzi ndi malo osinthila zovala

Malo opangira chakudya akhale ndi malo osinthira ndi zimbudzi zokwanila zoyenera zosavuta kupeza. Zimbudzi zimangidwe mwa ukhondo, kukhale kowala bwino, kopita mphepo, kotentha ngati kuli kofunika kutero komanso kusayang’anizane ndi malo okonzera chakudya. Malo ndi zipangizo zosambira m’manja omwe ali ndi madzi ofunda kapena otentha ndi ozizira, akhale pafupi ndi zimbudzi kuti aliyense ogwilitsa ntchito zimbudzizi adzidutsa pa malowa. Pa malopa pakhale zoumitsira m’manja za ukhondo. (monga makina a mpweya oumitsira manja kapena tinsalu taukhondo). Ngati tinsalu tikugwilitsidwa ntchito popukutira mmanja, tisinthidwe tsiku lililonse.

Posambira mmanja pa malo opangira chakudya 

Malo opangira chakudya akhale ndi malo osambira ndi oumitsira mmanja okwanila pomwe pakufunikira kutelo ndipo pakhale pomwe ogwira ntchito amadutsapo pochokera ku chimbudzi. Mhati pali poyenera, sopo apezeke pa malo osambira m’manja. Madzi ofunda kapena otentha ndi ozizira ndi uphungu wa kasambidwe koyenera zipelekedwe.

Maphunziro a za Ukhondo

Onse ogwira ntchito yopanga chakudya aphunzitsidwe bwino udundi wawo powonetsetsa kuti chakudya zisakhudzane ndi zinthu zomwe zingawononge chakudyacho ndi umoyo wa munthu. Amene amakonza chakudya akhale ndi chidziwitso ndi upangiri oyenera omwe ungawayenereze kukonza chakudya mwaukhondo. Onse ogwilitsa ntchito mankhwala oopsya aphunzitsidwe zoyenela kuchita.

Oyang’anira malo opanga chakudya kukhazikitsa ndondomeko zokwanira zophunzitsa ogwira ntchito awo akuti amvetse bwino za ukhondo wa pa malopo ngakhaleso wa pathupi pawo.

Ulamuliro ndi Kuyang’anira

Mkofunika kuti akulu akulu a malo opanga chakudya azikhala ndi nthawi yoyendera kuwonetsetsa kuti ndondomeko za ukhondo zikutsatidwa. Otsogolera ndi oyang’anira anzawo pa malo opangira chakudya ayenera kukhala ndi chidziwitso cha zofunikira pa zaukhondo, ndipo potsatira ndondomeko ya HACCP, apeze ndi kuzindikira ziopsezo ndi njira zopewera ziopsezozo.

Kuyezetsa matupi

Aliyense ogwira ntchito ku malo opangira chakudya akuyenera kuyezedwa ndi a chipatala asanalembedwe ntchito komanso pakatha miyexi isanu ndi umodzi (6) iliyonse kuwopa matenda opatsilana kudzera mu pweya ndi pokhudzana. Zikalata za umboni kuti anthu anayezedwa ndi dotolo ovomerezeka zikuyenera zisungidwe ngati dotolo waona kuti munthu sali oyenera kugwila ntchito pa malo opangira chakudya, munthuyo asaloredwe kugwira ntchito mpakana atapereka umboni osonyeza kuti wachira.

Matenda opatsilana

Atsogoleri aonetsetse kuti pasapezeke munthu oganiziridwa kuti akudwala matenda amene angafalikire kudzera mu chakudya, amene ali ndi zotupa ndi zilonda, tayifodi, kutsekula m’mimba mwa kamwazi, kutentha thupi, matenda opatsilana pogonana kapana matenda aliwonse amene ali opatsilana kapena amene angaononge chakudya, asagwire ntchito yopanga chakudya mwanjira ina iliyonse imene ingapangitse kuti munthuyo apereke chiopsezo pa chakudya. Ndi udindo wa ogwira ntchito aliyense kudziwitsa dotolo ngati pali wina ku banja kwawo akudwala matenda atchulidwa. Ogwira chakudya onse amene anachoka chifukwa anadwala ayezedwenso asanayambe kugwira.

Ukhondo wa munthu

Munthu wina aliyense ogwira zakudya ayenera kukhala waukhondo ndipo avale zovala zozitetezera komanso zobisa tsitsi ndi mapazi. Zinthu zonsezi zikhale kuti zikhoza kutsikidwa pokha pokha ngati zimatayidwa zikangogwilitsidwa ntchito. Zinthuzi zikhale za ukhondo nthawi zonse malingana ndi ntchito yomwe munthu akugwira.

Ma epuloni ndi zovala zina zofanana nazo zisachapidwire pansi. Munthu aliyense akhale ndi zovala ziwili zogwira ntchito kuti athe kusinthira. Zovalazi zingakhale bwino zitakhala za mtundu oyera chifukwa choti zimaoneka msanga zikada. Pa nthawi yomwe chakudya chikugwilidwa ndi manja, zibangili, mphete, kapena makoza amene sangatsukidwe ndi makhwala, zivulidwe. Ogwira ntchito asavale zozikometsera monga zingwinjiri, ma wotchi a pankono, ma phini ndizina zotero pamene akugwira chakudya.

Makhalidwe a munthu

Pogwira ntchito pa malo opangira chakudya, anthu apewe nkhalidwe lomwe lingaononge chakudya monga kutafuna zinthu (monga chingamu, mtedza, mitengo), kusuta fodya, kumina, kuvulala ndi makhalidwe ena a umve.

Kutaya Nyasi

Nyasi ziyenera kusungidwa mu njira yoti zisaononge chakudya kapena madzi oyenera kumwa. Samalitsani kuti tizirombo ndi nyama zoononga zisafikire nyasizi. Nyasi zichotsedwe pa malo opangira chakudya ndi malo ena pafupipafupi monga kuli koyenera, koma pasadutse tsiku zisanachotsedwe. Nyasi zikangotayidwa onetsetsani kuti ziwiya zones zomwe munali nyasizo zatsukidwa ndi mankhwala.  Malo osungapo nyasizo akuyenera atsukidwepo ndi mankhwala.

Ziwiya zonse zosungira kapena zonyamulira nyasi zisayandikile kumalo opangira chakudya.

Ziwiya zonse zosungira kapena kunyamulira nyasi zikhale zosiyana ndi ziwiya zosungiramo chakudya. Nyasizo zitayidwe tsiku lililonse. Zipangizo zolongedzera katundu, zoonongeka kapena zabwino, zisagwiritsidwe ntchito yosungiramo kapena kunyamulira nyasi.

Malo osungira nyasi akhale otchingika bwino kuti tizilombo ndi nyama zoononga zisathe kulowako kapena kuswana, zomwe zingaononge chakudya, ziwiya, madzi, nyumba ndi malo ena ozungulira malo okonzera chakudya.