Uchi umachokera ku njuchi. Popanga uchi ndi phula, zinyalala zonse zimachotsedwa mu uchi ongokololedwa kumene ndipo umalongedzedwa mu mabotolo olembedwa bwino. Uchi ndi ofunika pa thupi la munthu chifukwa umapatsa thanzi komanso umathandiza ku matenda osiyanasiyana. Phula la njuchi lomwe limapezeka mu uchi limagwiritsidwa ntchito ngati polishi opolishila zinthu zosiyanasiyana monga zitsulo ndi matabwa.
Zochotsera uchi mu zisa
- Zipangizo zochotsera uchi zina zimakhala za magetsi zina zapamanja koma zonsezi zimathandizila kulekanitsa uchi ndi zisa pozungulira
- Zipangizo zochotsera uchi zimakhala za milingo yosiyanasiyana ndipo zina zimakhala zazikulu kwambiri zotha kuchotsa uchi ku zisa 85 pa nthawi imodzi.
Makina ochotsera uchi amanja komanso amagetsi
Njira yosefa uchi
Njira iyi imakhala bwino kwambiri ku uchi omwe wakololedwa kumene
- Chotsani kaphula kapamwamba pa zisa kuti uchi utuluke ndi kusefedwa pa kansalu ka nayiloni kapena ka nsalu katimabowo ting’onoting’ono kukagwela mu ndowa yoyenela.
- Pindani kamodzi kansalu kanayiloni ndikukamangilila kukamwa kwa ndowa
- Ndowa yomwe igwiritsidwe ntchito posefa uchi ikhale ya kukamwa kwakukulu.
- Siyani Uchi udikhe kwa usiku umodzi.
- Chotsani kilimu pamwamba pa uchi ndipo longedzani mmabotolo.
Kusefa uchi
Kukonza uchi kugwiritsa ntchito madzi otentha
- Iyi ndi njira yomwe imagwiritsidwa ntchito pa uchi omwe wayamba kuuma.
- Poyambirira uchi umatenthetsedwa ndi madzi otentha. Mpoto omwe muli uchi umakhazikidwa mu poto wa madzi otentha kuti usungunuke.
- Uchi umayenera kutenthetsedwa ndicholinga choti usavute kusefa komanso kuti tizilombo tina ndi tina tife.
- Njira iyi imagwilitsa ntchito ma sefuliya awiri. Wamkulu ndi wam’ngono. sefuliya wamn’gono mumakhala uchi, wamkulu mumakahala madzi otentha omwe amatenthetsa uchi omwe uli mu sefuliya wamng’onoyo. Uchi omwe ukutenthetsedwa umayenera kutakasidwa kuti moto ufikire ponseponse.
- Uchi ukatentha umasefedwa pogwiritsa ntchito ka nsalu ka nayiloni.
- Uchi osefasefa udikhe kwa masiku atatu kenako ulongedzedwe.
Kutenthetsa uchi ndi madzi otentha
Kakonzedwe ka uchi ochuluka
Iyi ndi njira yomwe imagwiritsidwa ntchito pamene uchi wochuluka kwambiri ukukonzedwa pa nthawi imodzi.
- Munjira iyi uchi umadutsa pa ma sefa osiyanasiyana omwe ali ndi milingo ya mabowo yosiyana.
- Masefa amasanjidwa molingana ndi kuchepa kapena kukula kwa mabowo a sefa.
- Uchi otentha umadutsa mmasefa kuchokela mu ndowa yapamwamba kutsikira pansi ndipo umadikha kwa masiku atatu.
- Yalulani kilimu yemwe wayala pamwamba pa uchi ukadikha ndipo longedzani mmabotolo.
Kukonza uchi ochuluka pakamodzi.
Kufinya Uchi
- Mu njira iyi, uchi umafinyidwa kuchokera ku zisa pogwilitsa ntchito makina ofinyira.
- Izi zimachitika uchi ukangokoloredwa.
- Uchi ukafinyidwa, utenthetsedwe kugwilitsa ntchito madzi otentha ndi kusefedwa
Kusakaniza Uchi
- Uchi ochokera kosiyanasiyana umakhala ndi maonekedwe komaso makomedwe osiyana.
- Uchi ukuyenela kusakanizidwa kuti ufanane.
- Uchi osiyanasiyana ukuyenera kusakanizidwa ndi cholinga choti ukhale ofanana mmaonekedwe komaso makomedwe.
Kukonza Phula la njuchi
- Kulungani zisa zopanda uchi mu nsalu ya nayiloni
- Ikani poto wa madzi pa moto mpaka madzi atayamba kuwira pang’nopang’ono
- Ikani uchi okulungidwa mu madzi ndipo dikirani kuti zigaduke/zibwate
- Pamene madzi akuwira, zisa za uchi zisungunuka ndipo madzi asanduka chikasu.
- Pamene phula lawengeka, thirani mu ndowa ndipo siyani kuti lizizile ndi kuuma
- Phula lowuma limafunika kutsukidwa. Izi zimatheka poliwilitsa ndi kulisefa kangapo.