Module Articles

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

KUSAMALA CHINANGWA

Chinangwa si chakudya chokhacho chomwe chimapezeka pa mtengo wa chinangwa. Masamba a chinangwa amaphikidwa ngati ndiwo (chigwada). Thunthu losauma la mtengo wachinangwa ndi chakudya cha ziweto monga ng’ombe ndi mbuzi. Zitsa za mtengo wa chinangwa zimagwiritsidwa ntchito ngati nkhuni ndipo zina zotsalira pa mtengo wachinangwa zimagwiritsidwa ntchito ngati manyowa mu ulimi wa bowa. Chinangwa chimapatsa mphamvu ndipo chili mu gulu la zakudya zokhutitsa pa ma gulu a zakudya.

Chinangwa chachiwisi chimaonongeka msanga chifukwa chili ndi madzi ochuluka (65-70%) pamene ufa wa chinangwa okonzedwa bwino umakhala ndi madzi ochepa (10-12%) komanso umakhala nthawi ya itali. Chinangwa chimafunika kuchiyanika nsanga kuti ufa omwe udzapangidwe udzakhale wabwino.

ZOFUNIKA KOMANSO NDONDOMEKO

Zofunika

  • Chinangwa chachiwisi
  • Madzi
  • Mipeni
  • Greta
  • Choyanikira

Ndondomeko  

1:- Tsukani chinangwa mukangokolola kuti matope onse achoke.

2:- Sendani chinangwa ndi mipeni

3:- Nyenyani chinangwa kuti chiume nsanga

4:- Finyani chinangwa chonyenyanyenya ndi nsalu ya nayiloni kapena ndi makina (jack press)

Kunyenya chinangwa

 

5:- yanikani chinangwa  pa malo oyanikira okonzedwa mwa luso omwe amakhala ndi pansi patimabowo ting’ono ting’ono kuti mpweya uzilowa mosavuta ndi cholinga chokuti chinangwa chiume nsanga. (onani chithunzi mmusimu).

Poyanika chinangwa

 

6:- Chinangwa chowawa chikuyenera kuviikidwa m’madzi kwa masiku atatu kuti ma poizoni ena achoke. Kuviikaku pena kumapangitsa chinangwa kuyamba kusasa zomwe zimabweretsa ka fungo kangati ka mowa komwe anthu ena amakakonda.

7: Chinangwa chonyenyeka chouma chimagaidwa kupanga ufa.

8: Chinangwa chonyenyeka chithanso kulongedzedwa ndi ku gulitsidwa pachokha.

 

Kupanga Makaka

1: Tsukani chinangwa bwinobwino mukakolora

2: Sendani chinangwa pogwiritsa ntchito mpeni kapena makina.

3: Wumitsani chinangwa chosendasenda pa mphasa pa dzuwa kapena gwiritsani ntchito makina owumitsira a sola kapena magetsi

4: Chikauma, longedzani ndi kusunga malo owuma opita mphepo.

5: Chinangwa chowawa chikuyenera kuviikidwa m’madzi kwamasiku atatu chisanapangidwe makaka.