Mtedza ndi mbewu ya mgulu la nyemba yomwe ili yofunikira kwambiri kwa alimi muno m’Malawi. Mtedza umathandiza pankhani ya za chuma kwa alimi. Pandalama zomwe alimi amapeza kuchokera ku ulimi, pafupifupi theka limachokera ku mtedza. Mtedza ndiofunika kwambiri ngati gawo limozdi la chakudya kwa aMalawi chifukwa uli ndi michere yambiri yopatsa thanzi. Mu mtedza muli mafuta ndi zomanga thupi ngati zomwe zimapezeka mu nyama ndi mu mazira, pachifukwa ichi anthu omwe sangakwanitse kupeza mazira, nyama ndi mkaka akhonza kupeza michere yomweyo ku mtedza..
Mtedza umadyedwa wauwisi ophika kapena osaphika, ouma okazinga kapena osakazinga. Mtedza umakonzedwa kukhala nsinjiro kapenanso chiponde.
Chiponde chimapangidwa kuchokera ku mtedza owuma okazinga. Kawirikawiri mu chiponde mumathiridwa zinthu ngati mchere, shunga ndi zina zothandizira kuti chisungike nthawi ya itali. Pokonza chipode, mtedza umaphwanyidwa, kusankhidwa ndikukazingidwa kenako umasinjidwa mkusanduka chiponde.
1: Mtedza osaphwanya usankhidwe kochotsapo owola kapena odyedwa ndi tizilombo. Kusankha kumathandiza kuchepetsa aflatoxin (chuku) mu chiponde.
2: Kuphwanya mtedza. Mtedza umatha kuphwanyidwa ndi manja kapenanso ndi makina.
Makina ophwanyira mtedza
3: Ndikoyenera kusankha mtedza kuti tichotse mtedza owola, wa chuku, wobenthuka, wodyedwa ndi tizilombo komanso wosintha mtundu. Kusankha mtedza kumathandiza kuti chiponde chikhale cha mtengo wapatali komanso osapeleka chiopsezo pa moyo wa munthu. Mtedza obenthuka umapserera msanga pokazinga zomwe zimasokoneza makomedwe ndi fungo la chiponde ndi chifukwa chake kuli koyenera kuuchotsamo.
4: Kupeta kumathandizira kuchotsa fumbi komanso zinyalala ku mtedza. Miyala, fumbi ndi makoko amatha kupezeka mu mtedza wokuswa kale ndipo zitha kuononga chiponde.
5: Kukazinga mtedza. Kukazinga mtedza kumaphweketsa ntchito yosupula. Kusintha kwa mtundu kwa mtedza pena sikuonekera pakhungu.pachifukwa ichi nkofunika kusupula mtedza ndi kugamphula pakati kuti uoneke bwino.
6: Kusankha ndi kupeta. Izi zimachitika ndicholinga chochotsa makungwa, mitima ndi mtedza wosintha mtundu. Mitima imapsyelera msanga pokazinga ndipo nkoyenera kuichotsa kuti chiponde chikhale chabwino.
7: Kazingani mtedza pa moto wa 1900C kwa mphindi khumi ndi zisanu (15) mpaka utapsa bwino.
8: Ngati mwakonda kutero sakanizani supuni imodzi yaying’ono ya mchere ndi ina ya shuga pamodzi ndi mtedza okwana ma kilo khumi (10kgs).
9: Gayani mu makina opangira chiponde.
Makina opangira chiponde
10: Longedzani mu mabotolo a ukhondo.