Module Articles

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

Kukonza Ndi Kusamala Zokolola

KUSAMALA MPUNGA

Msika wa mpunga m’madera ambiri umayendetsedwa ndi ma venda chifukwa palibepo misika yokhazikika ya mbewuyi. Magulu ambiri a alimi ampunga alibe zowayenereza kusunga kapena kupuntha mpunga. Pachifukwa chimenechi iwo amakhala okakamizika kugulitsa mpunga wawo kwa mavenda. Kupuntha mpunga ndi njira imodzi yapafupi yomwe alimi angatsate kuti azigulitsa mpunga wawo pa mtengo wokwera.  Popuntha mpunga, chikhungwa ndi madeya zimachokera limodzi poteropo kutulutsa mpunga woyera.

Ndondomeko yopuntha mpunga

Zofunikira ndi Ndondomeko

  • Mpunga osapuntha
  • Chigayo cha mpunga
  • Makina ochotsera miyala
  • Makina osankhira ndi kuikira mmagulu 
  • Zipangizo zolongedzera

Ndondomekeo  

1:  kuchotsa makungwa

Mpunga osapuntha umayenela kupunthidwa kuti makungwa komanso madeya achoke. Tikachotsa makungwa timapeza mpunga  wa brown. Makungwa ochotsedwawo  atha kugwiritsidwa ntchito ngati nkhuni komanso kuyika pansi mu makola aziweto monga nkhuku.

Makungwa a mpunga ndi nkhuni zokonzedwa kuchikera ku makungwawa.

2: Kupolisha (kuchotsa deya wa mpunga)

Popolisha mpunga, madeya ndi mitima zimachotsedwa pa mpunga wa brown. Mpunga opolishidwa umakhala woyera mbee ndipo madeya ampunga ndi mitima zimatuluka pazokha kuchigayo cha mpunga. Madeya a mpunga ndi a mtengo wapatali chifukwa amagwiritsidwa ntchito ngati zakudya za ziweto. Mu madeya a mpunga muli michere yomanga thupi, mafuta ndi michere ina yofunikira ku ziweto.

Madeya a mpunga

3: Kuchotsa Miyala

Iyi ndi ndondomeko yochotsa miyala ndi zina zosafunika kupezeka mu mpunga pogwiritsa ntchito makina. Pamapeto pochotsa miyala timakhala ndi mpunga pawokha komanso miyala payokha.

Mpunga opanda miyala

 

4: Kusankha  

Iyi ndi ndondomeko yosankha mpunga. Mpunga opuntha umatha kukhala ndi mpunga wa mpumphu, mpunga wobenthuka mosiyanasiyana, madeya komanso fumbi. Pamapeto pa ndondomeko iyi, mpunga umakhala wamphumphu pawokha, wobenthuka pawokha..

Step 6: Kulongedza

Pomaliza, mpunga ukuyenera kulongedzedwa mmapepala ndi kumatidwa bwino kapena m’matumba ndipo zikatero mpungawo ukhonza kupita ku msika.

Mpunga wa kilombero wa mpaketi