MAWU OYAMBIRIRA
Mbatata ya Kachewere ili ndi kuthekera kwakukulu kothandizira kupanga ndalama, kubweretsa chakudya cha pakhomo, kuthandizirapo chitetezo cha mthupi komanso kupereka mphamvu yokhala ndi moyo wozidalira tokha ngati a Malawi. Kachewere atha kulimidwa kwa chaka chonse kuno ku Malawi.
Cholinga Chachikulu
Kupititsa patsogolo chidziwitso ndi luso pakati pa alimi ang'onoang'ono pa ulimi wa Kachewere. Kuonjezera apo, cholinga china ndi kusintha miyoyo ya anthu powonesesa kuti chakudya chikupezeka m’makomo komanso ndalama zomwe alimi angapeze mu ulimi wa Kachewere.
Pamapeto pa gawoli, alimi azitha kupanga izi:
ZOFUNIKIRA KUTI KACHEWERE AMERE BWINO
Zofunikira mu dothi
Zofunikira zokhudza kafundidwe
MITUNDU YOVOMEREZEKA
Chuma
Maonekedwe: Yokhala ndi khungu lofiyira losalala, yowoneka ngati yozungulira, yachikasu ndi timadontho ting’onoting’ono mkati
Maonekedwe a Mbewu: Mtundu wautali wokhala ndi tsinde lowonda komanso yokhala ndi maluwa oyera
Kagwirisidwe ntchito: Tchipisi
Kupilira ku matenda: Imapilira kwambiri ku chiwawu komanso tizilombo.
Kucha : imachedwerapo kucha (imatenga masiku osachepera 90 komanso osaposera 120)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu osachepera 14,000 -16,000 pa Ekala
Violet
Maonekedwe: Yaitali komanso imaika mbatata ikuluikulu, Khungu lofiilira komanso mkati mwa chikasu chotuwilapo. Imakhala ndi mphukila zoonekelatu
Maonekedwe a Mbewu: Mtundu wautali wokhala ndi tsinde lowonda komanso yokhala ndi maluwa oyera
Kagwirisidwe ntchito: tchipisi
Kupilira ku matenda: Ndiyosapilira ku chiwawu.
Kucha: imatenga masiku osachepera 90 komanso osaposera 105
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu 10,000-12,000 pa ekala
Rosita
Maonekedwe: Ili ndi khungu lofiyira, yaitali maonekedwe, mbatata yake imaika yokulilapo komanso ikuluikulu. Yachikasu mkati ndi timaso timaso
Maonekedwe a Mbewu: mkhalatsonga ndi yotalikilapo ndi masamba amphamvu obiriwira. Imatulutsa maluwa ochepa ndipo maluwawo amakhala oyera ndi utoto wofiirira
Kagwirisidwe ntchito: tchipisi
Kupilira ku matenda: Ndiyosapilira ku chiwawu.
Kucha: Imacha mwachangu (masiku 90)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu 7,000-10,000 pa ekala
Thandizo
Maonekedwe: Mbatata ya khungu loyera/kirimu, mkati mwa chikasu motuwa, mbatata yozungulira
Maonekedwe a Mbewu: Zomera zapakatikati mpaka zazitali zomwe zimaphuka kwambiri; makamaka maluwa oyera
Kagwirisidwe ntchito: Tchipisi
Kupilira ku matenda: Ndiyopilira ku chiwawu komanso tizilombo
Kucha : Imacha mwachangu (masiku 90)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu 14,000-16,000 pa ekala
Zikomo
Maonekedwe: Mbatata ya khungu loyera/kirimu, mkati mwa chikasu motuwa, mbatata yozungulira
Maonekedwe a Mbewu: Mkhalatsonga, siitalika kwambiri, nthambi zamphamvu, masamba otambalala otuwilapo obiliwira, maluwa ofiilira
Kagwirisidwe ntchito: Tchipisi
Kupilira ku matenda: mbewuyi imapilirako ku chiwawu ndi tizilombo
Kucha : Imacha mochedwa (masiku 90 - 115)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu14,000 pa ekala
Mwai
Maonekedwe: Mbatata yozungulira zakhala ndi khungu lofiilira, mkati mwa chikasu motuwilapo ndi timaso timaso
Maonekedwe a Mbewu: Mkhalatsonga yotalikilapo ndi nthambi za mphamvu.
Kagwirisidwe ntchito: Tchipisi
Kupilira ku matenda: mbewuyi imapilirako ku chiwawu ndi tizilombo tambiri
Kucha: Imacha mochedwa (masiku 90 - 120)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu osachepera 14,000 pa ekala
Lady Rosetta
Maonekedwe: Mbatata yozungulila, ya khungu lofiila ndi maso osalowa kwambiri otayana mofanana, ili ndi nsidze zoonekela kwambiri, mkati mwake mwa chikasu motuwira.
Maonekedwe a Mbewu: Ili ndi nthambi zitalizitali, komanso chiwerengero chabwino cha tsinde zapakati. Ili ndi masamba obiriwira kwambiri
Kagwirisidwe ntchito: Tchipisi
Kupilira ku matenda: Mbewuyi ndi yosachedwa kugwinda ndi chiwawu
Kucha: Imacha mochedwa (imatenga masiku 110 – 120 kuti iche bwino)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu osachepera 12,000 pa ekala
Mtukulapakhomo
Maonekedwe: Mbatata yozungulira komanso ya khungu la kirimu. Yoyera mkati
Maonekedwe a Mbewu: Mkhalatsonga yotalikilapo ndi masamba obiriwira. imatulutsa maluwa mochepa ndipo zimakhala ndi maluwa apakati.
Kagwirisidwe ntchito: Yabwino kuphika, kukazinga komanso ku kasha
Kupilira ku matenda: mbewuyi imapilirako ku chiwawu
Kucha : Imacha mofulumirapo (masiku 90 - 110)
Kuthekera kwa zokolola: titha kukolora ma kilogalamu osachepera 12,000 pa ekala