KUKOLORA / KUKUMBA KACHEWERE
Alimi kukolora / kukumba ndi kuyika mmatumba Kachewere
Fundo Zoyenera kudziwa pakakololedwe ka Kachewere
- Nthawi ya Kucha: imakhala pakati pa miyezi 3 – 4 mutadzala kutengera mtundu
- Mbatata zomwe zimakololedwa zisanakhwime zimakhala zazing’ono, ndipo zimakhala ndi khungu losakhwima, zomwe zimatha kupangitsa kuti palowe tizilombo toyambitsa matenda.
- Komabe, Kachewere yemwe walimidwa ngati mbewu amakololedwa msanga, pofuna kupewa matenda ofalitsidwa ndi virus omwe angayambe kumapeto kwa nyengo yolima.
Mfundo Zofunika:
- Kachewere aphimbidwe ndi dothi kuti muchepetse kubiriwira komanso kulowa kwa njenjete za mbatata
- Kudula masamba patatsala masabata awiri musanakolole kumakhwimitsa khungu la Kachewere. Kuumitsa kwa khungu kumachepetsa kuwonongeka kwa Kachewere wanu panthawi yokolola ndi kusunga
- Kachewere wokumbidwa ayenera kusungidwa mwaukhondo, pa malo owuma, akhale wa khungu lokhwima lopanda mabala, tizilombo toononga komanso matenda.
- Kuti asawole, musamutsuke Kachewere ndi madzi, koma koma mutha kumupukuta kuti muchotse dothi ndikumu sunga pamalo ozizira ndi owuma.