KASAMALIDWE KA MBEWU
Kubandira/Kukwezera mizere
- Izi zimapangidwa kuti tiphimbe mbatata ndi dothi lokwanira
- Izi timapangira limodzi popalira munda
- Kukwezere mizere komaliza kukuyenera kuchitika mbewu isanayambe kutulusa maluwa
- Osakwezera mizere mvula ikagwa kumene kapena dothi likakhala lonyowa
- Mzere okwezeredwa bwino umachepetsa tchire, umachepetsa kusakhwima bwino kwa Kachewere, umachepetsa matenda komanso umapangitsa kuti kukumba mbatata pokolola kusazavute.
Munda wa Kachewere wa mizere yokwezeredwa bwino