KUTHANA NDI TIZILOMBO NDI MATENDA A KACHEWERE
Kasinthasintha wa malo olima mbewu
- Imodzi mwa njira zofunika kwambiri pa kupewa matenda a Kachewere ndi kusinthasintha wa malo olima
- Kasinthasintha wa malo alima kumateteza kuti tizilombo toononga komanso matenda tisachulukane. Komanso kumapangitsa kuti nthaka ikhale ya thanzi.
- Ndibwino kuti musinthanitse mbewu podzala mitundu ya mbewu zina yosiyanasiyana; pulogalamu yosintha mbewu yabwino ikhale posintha mtundu wa mbewu pakadusa zaka zitatu kapena zinayi.
Zilombo zowononga zikuluzikulu
Tizilombo timawononga zokolola. M'munsimu muli tizilombo towononga Kachewere kuno ku Malawi:
Njenjete za Mbatata (Potato Tuber Moth)
Njenjete pamwamba pa mbatata
chowonongedwa ndi Njenjete
Zizindikiro:
- Njenjete ndi yaying'ono, yobiriwira imvi ndi mapiko opapatiza
- Njenjete zimaononga kwambiri makamaka cha kumadzulo
- Mbozi zake zili mpaka ma millimita 12 mulitali, zakhala ndi mtundu oyererapo kapena owezuka
Zomwe Njejete Zimaononga:
- Zimaboola mkati mwa mbatata kupanga tinjira tomwe timathanso kulowetsa matenda ena mbatata ikamaola
- Tingalande topangidwato timapangisa kuti Kachewere akhale osadyeka ndi anthu.
- Tizilomboti timasunthidwa limodzi ndi zokolora zomwe zimapasira matenda ku zokolora zina
Kupewa/Kuthanna ndi Njenjete
- Gwiritsani ntchito mbewu yabwino komanso yopanda matenda chifukwa mbewu yowonongeka ndiyomwe imayambitsa kuononga zinzake m'munda.
- Dzalanu pataliko mu nthaka (mulingo wabwino ukhale ma centimita osachepera 10) komanso yesesani kukwezera mizere kosachepera katatu
- Kukweza mizere kwambiri ndikofunika chifukwa zimakanikisa njenjete kukwera mizere ndi cholinga choti zifikire pa mbatata ndikuikira madzira.
- Chotsani zolokola zones mmunda kusanayambe kuda kuti njenjete zisaikire madzira
- Osasiya zokolora mu m’dima usiku onse zitakoloredwa
- Gwirisani ntchito mankhawala othamangitsa njenjete kuti zikanike kufikira mbatata monga Lantana camara and Eucalyptus.
Nsabwe za m’masamba
Nsabwe pamwamba pa tsamba ta Kachewere
Zizindikiro:
- Pali mitundu yosiyanasiyana yomwe imazunza mbewu ya Kachewere monga green peach aphid, potato aphid & cotton aphid
- Nsabwezi zimapezeka makamaka kunsonga komanso kunsi kwa tsamba la mbewu
Zomwe Nsabwe Zimaononga:
- Kudya kwa nsabwe kumapangisa kuti masamba akule monyetchera.
- Nsabwezi zimasiya tiuchi mmasamba ndipo kachilombo ka virus kamafalikila mozungulira tiuchiti
- Nsabwezi zimafalitsanso Nthenda ya Potato Leaf Roll Virus imene ndiyovuta kwambiri mu ulimi wa Kachewere
Kupewa/ Kuthana ndi Nsabwe
- Kugwirisa ntchito mankhwala monga
- Nuprid 200 SC® (a.i. Imidacloprid)
- Karate 2.5WG® (a.i. Lambda Cyhalothrin)
- Phatikizani zomata kuti mutchere nsampha nsabwezi
- Tetezani kwambiri Kachewere yemwe mwamlima ngati ochulukitsa mbewu ku nsabwe
- Dzalanu mbewu pa muyezo wabwino
Root Knot Nematode (Tinyongolotsi tosaoneka ndi maso)
Zizindikiro:
- Izi ndi tizilombo ting’onozing’ono tosaoneka ndi maso tomwe timakhala mu dothi
- Nyongolotsizi zimatha kuzindikiridwa ndi zizindikiro zomwe zimaoneka mu Kachewere
- Nyongolotsizi zimakonda malo ndipo matendawa amakhazikika kwambiri mu Kachewere olimidwa mmadera otentherapo
Zomwe Nyongolotsizi Zimaononga:
- Kunyentchera kwa Kachewere kosiyanasiyana, chikasu m’masamba ndi kuuma kwa mbewu mwachangu madzi akachepa
- Kutupa ngati ka mpira m’ mitsitsi
- Khungu la mbatata limakhala lokhakhala
- Madonthomadontho oderapo mkati mwa mbatata mukaipala khungu pang’ono
- Nyongolotsizi zimafalikira kwambiri mu mbatata zowonongeka kale komanso mu dothi lomwe lagwidwa nazo
- Nyongolotsizi zimawonjezera matenda ofalitsidwa ndi bacterial ndi komanso matenda ena
Kupewa/ Kuthana ndi Root Knot Nematodes
- Kusinthasintha malo olima mbewu zosiyanasiyana
- Nthaka ya chonde ndi manyowa ambiri (manyowa, kompositi & "Bokashi" etc.)
- Kukataya / kuwononga zotsalira za mbewu
- Kugwiritsa ntchito mankwala, monga
- Bio Nematon (The biologide Nemalogide)
Akangaude
Zizindikiro:
Pamaso, akangaude amaoneka ngati timadontho ting’onoting’ono koma tizilomboti timatha kuwoneka pogwiritsa ntchito galasi lokuzira tizinthu tating;ono kuti tionrke bwino (Magnifying glass)
- Amakhala m'magulu, makamaka kunsi kwa masamba ndipo amaluka ukonde wa kangaude
- Akangaude akuluakulu ali ndi miyendo 8 ndi thupi lozungulira lomwe lili ndi madontho awiri pamutu pake
- Mazira amakhala obulungika komanso owoneka bwino amakhala amtundu wa kirimu asanaswe
- Tizilomboti timawononga nthawi yotentha komanso kouma
Zomwe kangaude amaononga:
- Kangaude amawononga poyamwa ma madzi a masamba
- Poyamba, kuwonongeka kumawoneka ngati madontho opepuka pamasamba omwe nthawi zina amakhala ndi utoto
- Pakupita kwa nthawi masamba amasanduka achikasu ndikugwa
- Nthawi zambiri, masamba ndi tsinde zimakutidwa ndi ukonde wa kangaude wambiri
- Kuwon nthawi zambiri zimakhala zovuta kwambiri zikaphatikizidwa ndi kupsinjika kwa madzi
Kupewa/ Kuthana ndi Akangaunde
- Thirani mankhwala oyenera omwe amapha magawo osiyanasiyana a kangaude (kuyambira mazira mpaka tizilomba tikulutikulu) monga mankwala awa:
- Hattrick EC® (a.i. Oxydemeton-Methyl)
- Pofuna kupewa tizilombo ting'onoting'ono kuti tisazolowere mankwala, kasinthasintha wa mankhwala omwe ali ndi kapangidwe kosiyanasiyana kumathandiza
Nyongolotsi zomwe zimadula mbewu - Cutworms
Zizindikiro:
- Ana a nyongolotsizi amakhala mu nthaka ndipo amadula mitsinde nthawi ya usiku
- Tizilomboti timawononga kwambiri nthawi yomwe kunja kwauma
Zomwe ma Cutworms amaononga:
- Ma Cutworms amadya mbatata ndi mizu, amabowola ndikusiya bowo lalikulu losazama kwambiri
- Ndi tizirombo towopsa kwambiri ku Kachewere yemwe wangophukira kumene, ndipo timatha kuwononga mbali yayikulu ya munda.
Kupewa/ Kuthana ndi ma Cutworms
- Kulima komanso kutola ndi manja
- Konzani m'munda ndikuwononga tchire lonse masiku 10 mpaka 14 musanadzale
- Kulima kumathandiza kuika poyera pa dzuwa tiziloboti ndipo zikatero timafa ndikutentha kwa dzuwa
- Kuthira madziochuluka m’munda(Flooding) musanadzalidwe kutha kuthandiza kupha tizilomboti tomwe tili mu dothi.
Matenda
Chiwawu chochita Kachewere ataika kale (Late Blight)
• Awa ndi matenda a fangasi omwe amakonda kuchitika kwambiri nthawi yozizira ndi yamvula
• Ndi imodzi mwa matenda owononga kwambiri Kachewere
Zizindikiro:
- Masamba ake amakhala ndi timadontho ngati panyowa omwe amakula ndi kusanduka bulauni
- Pansi pa tsambalo, pamasanduka nkhungu zoyera zomwe zimawonekera m'mphepete mwa tsambalo
- Masamba okhudzidwawo amafota, koma nthawi zambiri amakhala pa tsinde
Kupewa / Kuthana ndi Late Blight
- Kuli bwino kudzala mbewu zopilira ku matenda monga “Zikomo”/ “Chuma”
- Kudzala mbewu mwa kasinthasintha wa malo kumathandiza kupewa matendawa (Crop rotation)
- Yesetsani kukhala awukhondo popanga pozula ndi kuonongeratu mbewu iliyonse yopezeka ndi matenda
- Sankhani mbewu zoti sizimagwidwa ndi matenda
- Thirani mankhwala oyenerera onse opewera ndi ochizira matendawa
Bacterial Wilt /Thuku / Getsi
- Matendawa amayamba ndi bakiteriya wotchedwa Pseudomonas solanacearum
- Ndi matenda owopsa kwambiri omwe amatha kuwononga munda wonse
- Tizilombo toyambitsa matenda timakhala m'nthaka kwa nthawi yayitali ndipo timalowa mmbewu kudzera m'mabala amizu ndi tsinde la tsinde.
- Matendawa amafala ndi mbewu ya mbatata yomwe ili ndi kachilombo kale
Zizindikiro:
- Kachewre yemwe wagwidwa matendawa amanyala ngakhale munthaka muli chinyezi chokwanira
- Kunyala kumachitika mwachangu ndipo munda onse Kachewere amafa m'masiku ochepa
- Zotuluka zoyera kuchokera ku mbatata kosalekeza kumatuluka mmaso mwa mbatata zomwe zakhudzidwa
Kupewa/ Kuthana ndi Bacterial wilt
- Kugwiritsa ntchito mbewu yopanda matenda
- Phunzirani kasinthasintha wa malo olima mbeu (zaka 2 - 3) zulani ndi kuonongeratu mbatata zongomera pazonkha zomwe zingatuluke
- Kuotcha zinyalala ndi tchire za mmunda womwe wakhudzidwa
- Pewani kubweretsa dothi lochokera mmunda okhuzidwa ku munda watsopano
- Pewani kudula mbatata ngati njira yochulutsa mbeu mukakhala ndi mbatata yosakwanira
- Thilani 10 % ya sodium hypochlorite (bulichi) pa mbewu imodzi imodzi yogwidwa ndi matendawa pamene mukuyendera mmunda wanu
-
Chiwawu cha koyambilira – Early Blight
Zizindikiro zoyambirira za Chiwawu
• Matendawa amayambika chifukwa cha fungasi otchedwa Altenaria solani
• Fungasi amatha kukhala mu zinyalala ndi tchire la mminda yokhudzidwa kwa zaka zingapo
• Matendawa amachita bwino malo omwe ali ndi chinyontho komanso ofundirapo
Zizindikiro:
- Choyamba, mawanga ozungulira kapena aang'ono oderapo amawonekera pa tsamba la Kachewree
- Nthawi zambiri, malo okhakhala amakhala patsambapo ndipo limalowererana ndi kubiriwira kwa tsambalo
- Masamba oti agwidwa kwambiri ndi nthandayi pakadusa nthawi amagwa okha
Kupewa / Kuthana ndi Chiwawu (Early Blight)
- Kugwiritsa ntchito mbeu yopanda matenda
- Ukhondo wabwino wa m'munda pogwiritsa ntchito rouging
- Yesetsani Kasinthasintha wa mbeu
- Kuwononga zotsalira za mbeu zomwe zakhudzidwa
- Gwirisani ntchito mankhwala oyenera ophera chiwawu
Bacterial Soft Rot ( Matenda oworetsa mbatata)
• Matendawa amayamba chifukwa cha bakiteriya: Erwinia spp.
• Amalowa m'nthaka kudzera m'mabala a masamba kapena tsinde pafupi ndi nthaka
• Matendawa amachita bwino ndikukhala owopsa mu malo otentha a chinyontho
• Bakiteriya amafalikira ndi mvula
• M'minda yamadzi ambiri mu dothi lake, mbatata zimawola
Mbatata yogwidwa ndi Bacteria Soft Rot
Zizindikiro:
- Tsinde ndi masamba zimatuluka zotupa zomwe zimadzadzidwa ndi madzi, pamapeto pake zimawola ndi fungo loipa.
- Pa mbatata, timadontho tofiira tabulauni timapanga pa mphodza
- Zigawo zamkati za machubu zimawoneka zowola zofewa komanso zotsekemera zimawonekera ndipo zimatha kuwola panthawi yoyendetsa kapena kusungidwa m'malo mopanda mpweya wabwino, kutentha kwambiri komanso chinyezi.
Kuthana / Kupewa Bacterial Soft Rot
- Yesetsani kasinthasintha wa malo olima mbeu ndi mbewu monga chimanga
- Kugwiritsa ntchito mbewu yabwino ya mbatata
- Onetsetsani kuti mmunda mwanu muike ngalande zochotsa madzi
- Sungani ndi kunyamula mbatata mu malo owuma,ndi a mpweya wabwino
- Ukhondo m’munda mopanda tchire
- Kusankha bwino zokolora; zowola musanalongeze mukakolora
Potato Leaf Roll Virus (PLRV)
- Awa ndi matenda a Kachewere omwe amapezeka m’madera onse omwe amalima Kachewere
- Amafalikira ndi nsabwe za m'masamba.(Aphids)
- Kachilomboka kamafalanso kudzera mmbewu yamatenda komanso Kachewere ongomera yekha yemwe zili ndi matendawa
Kachewere wa matenda a PLRV pafupi ndi Kachewere opand matenda
Zizindikiro:
- Kachewere yemwe matendawa akufalitsidwa ndi nsabwe za m'masamba, masamba amapindikira m'mwamba
- Kachewere yemwe matendawa amafalikila chifukwa chodzala mbewu ya matenda kale, masamba apansi amapindikira mmwamba (akamera) ndikukhala ngati supuni.
- Masamba okhudzidwa kwambiri amapindikilatu kupanga ngati kanjira kozungulira pakati
- Kachewere amapinimbira ndipo amaika mbatata ing’onoing’ono
- Ngati timbatatati tidzalidwanso ngati mbewu, Kachewere wake amakhala opinimbira ndipo saika bwino
Kupewa /Kuthana ndi PLRV
- Kugwiritsa ntchito mankhwala pofuna kuthana ndi nsabwe za m'masamba zomwe zimatha kufalitsa kachilomboka ku zomera za mbatata monga
- Nuprid 200 SC (a.i. Imidacloprid)
- Karate 2.5WG (a.i. Lambda Cyhalothrin)