ZOFUNIKA KUTSATA PODZALA MBEWU
- Kachewere amadzalidwa kuchokera ku mbatata ndipo amadzalidwa bwino mumizere
- Mbatata iyenera kukhala ndi ‘diso’ limodzi kapena mphukira. Siyani ma mbatata pamalo amthunzi kwa sabata imodzi kapena ziwiri musanabzale kuti mphukira ziwumitsidwe.
- Dzalani mbatata zomera bwino ndikuwonetsetsa kuti mphukira zaloza mmwamba.
- Dzalani mbatata mozama 5cm pansi ndi 30cm motalikirana ndi mzake
- Dzalani Kachewere itangogwa mvula yoyamba.
- Kachewere amakula bwino akadzlidwa pa munda osaphatikiza mbewu ina iliyonse.
Miyezo ya Feteleza:
- Podzala, wazani kaye D Compound ndikuphimba fetelezayo bwinobwino ndi dothi lokwana 5 cm
- Mukadzala mbatata yanu, muyenela kuthira feteleza pasanathe sabata imodzi
- Mlingo uyenera kukhala motere: makilogalamu 80 pa ekala limodzi
- Ikani magalamu 15 pa phando, ikani feterezayo ma centimita 5 patali ndi mbewu
- Mukhozanso kugwiritsa ntchito manyowa
- Pakatha masabata atatu, thirani fetereza okulitsa wa CAN pamulingo wa 80Kg pa ekala iliyonse.
Zindikirani:
Musagwiritse ntchito Feteleza wa UREA chifukwa ali ndi mchere wa Nitogen wochuluka popeza umalimbikitsa kukula kwa zomera ndi kuwononga kaikidwe ka mbatata.
Zofunikira zokhudzana ndi Madzi
- Kachewere amafuna mvula yapakati pa ma millimita 850 mpaka ma millimita 1,200 pa nthawi yomwe Kachewere yu akukula.
- Chinyezi chochepa komanso chosinthasintha chimapangitsa mbatata yomwe ikuika kuti ionongeke.
- Kuthirira nthawi ya m’mawa komanso chakumadzulo ndikolimbikisidwa chifukwa kumathandiza kuchepesa kuuluka kwa madzi kudzera mmasamba chifukwa cha dzuwa.
Kasamalidwe ka Udzu Omera
- Kupalira mokwanira kumafunika kuti pakhale zokolola zambiri
- Mutha kulapira ndi manja
- Kupalira kuchitike tchire likamera kumene kupewa kudzula limodzi ndi mbatata yoti yayamba kuika.
- Kupalira koyamba: pakapita sabata imodzi kapena awiri Kachewere akatuluka
- Kupalira kachiwiri: pakapita masabata anayi kapena asanu mbewu zikamera.
- Osapalira nthaka ikanyowa kuti dothi lisasinjike
- Mbewu zikaphuka masamba ake amabisa mizere yonse ndipo izi zimathandiza kuchepetsa tchire.
Munda wa Kachewere opalilidwa bwino