KUSANKHA MBEWU NDI KUKONZA MUNDA
Kusankha Mbewu
- Alimi a Kachewere akuyenera kusankha mbewu yoti adzale ulendo otsatira pomwe Kachewere akadali mmunda. Iyi ndi njira yabwino kwa kanthawi kochepa.
- Mbewu yabwino mmunda imayamba ndi kusankha mbeu yabwino yoti idzalidwe
- Yang'anani mbeu kuti muwone ngati ili ndi zizindikiro za matenda
- Mbewu za matenda zisasankhidwe
- Mbewu zabwino zomwe zasankhidwa piikidwe ka mtengo koonekera patali ngati chizindikiro
- Gwiritsani ntchito mbeu yopanda matenda
- Kukula kwa Kachewere kukhale kolingana ndi kukula kwa dzira la nkhuku
- Pezani mbewu zatsopano zodzala pazaka zitatu zilizonse
- Nambala ya mphukira ikhale yosachepera zinayi
Alimi Kusankha mbeu ya Kachewere
Mbewu zoyamba kumera
Kukonza Malo Olimapo
Zofunika kutsata pokonza malo Olima:
- Malo omwe mukulimapo Kachewere akhale oti sipanalimidwe mbewu ina yoti imagwidwa ndi matenda ofanana nayo maka tizilombo topezeka mdothi monga monga ma nematodi
- Dothi lilimidwe bwino kuti muchotse udzu, zibungwe komanso kuti mpweya uziyenda bwino.
- Pangani mizere yokwera 30cm kuchokera pansi, ndipo pakhale mpata wa pakati pa 75cm ndi 90cm kuchoka pa mzere wina
- Mbatata idzalidwe mmizere
- Chotsani zomera zina m’munda pofuna kupewa kufala kwa matenda
- Kukwiliranso zotsalira za mbewu m'munda kungathe kuonjezera kwambiri nthaka