Module Articles

Kachewere

Kachewere

Kasamalidwe ka zokolola

MOMWE TINGASAMALIRE ZOKOLORA TIKAMALIZA KUKOLORA

Monyamulira ndi Kusungira Kachewere

  • Kachewere akuyenera kugulitsidwa m'matumba a 50 kg m'misika
  • Kapena mu ndowa olo mabigili oyeza bwino

Katundu wina yemwe angathe kupangidwa kuchokera ku Kachewere:

Kutsuka, Kusankha. kusanthura ndi Kusonthora

1. Kusankha:

  • Kachewere yemwe ali ndi matenda, woduka, komanso osaoneka bwino, amatayidwa kuti asakhale pamodzi ndi Kachewere wabwino

2. Kuyika ma gulu a maonekedwe osiyana:

  • Kachewere amasankhidwa malinga ndi kukula ndi mawonekedwe
  • Mbatata zimagawidwa motere:
    • Wamalonda:>  ma milimita oposera 55
    • Wambewu: ma milimita oposera 45 koma osaposera 55
    • Wambewu: ma milimita opesera 25 koma osaposera 35
    • Otsalira: Osakwana 25 milimita (Imagwiritsidwa ntchito ngati chakudya cha ziweto)

 

Kasungidwe

  • Kachewere wa Malonda :
    • Kachewere ayenera kusungidwa m'malo amdima kuti asamere
    • Malo osungila ayenera kukhala wozizira komanso podutsa mphepo yabwino
  • Kachwewere wa Mbewu
    • Kachewere amasungidwa m'malo ozizira ndi kuwala kowoneka bwino kuti iziphukira mobiliwilira, komabe pewani kuwala kwa dzuwa kuopa kuononga mbewu.
  • Kachewere amathanso kusungidwa kwa nthawi yayitali poyiyika pa nyenyeswa za zopala za matabwa,  m'chipinda cha mpweya wabwino chomwe sichilowai dzuwa lambiri.
  • Kachewere amatha kusungidwa kwa miyezi 1-2 isanamere, mukamusunga bwino.
  • Kachewere yemwe wasungidwa aziwonedwa sabata iliyonse kuti tidziwe momwe zilili.
  • Mbatata zowola zonse zizichotsedwa

 

Kuyamikira ndi

Izi zidalembedwa ndi bungwe la Farm Concern International (FCI) mogwirizana ndi ogwira ntchito ku unduna wa zamalimidwe ku Lilongwe. Zomwe zalembedwazi zachokera ku Centre for International Potato (CIP) Malawi & Mr. Given Kalonga