Module Articles

Mtedza

Mtedza

Mitundu

Mitundu (Chichewa)

Chalimbana -  

Umagwiritsidwa ntchito ngati nsinjiro, umachita bwino m’madera ambiri okwera.

Mtedzawu ndi waukuluukulu ndipo umakhwima pakatha miyezi inayi ndi isanu kuchokera tsiku lobzala.

Chitembana

Umangwiritsidwa ntchito ngati nsinjiro, umaoneka ozungulira komanso ukulu ukulu ndipo umafananako ndi Chalimbana. Umakula bwino Madera onse okwera monga chalimbana. Umakhwima pakatha masiku a pakati pa 130 mpaka 150 kuchokera tsiku lobzala.

CG7

Umagwiritsidwa ntchito ngati nsinjiro, umaoneka okulirapo. Umacha msanga. Umakhwima pakati pa miyezi inayi ndi isanu kuchokera tsiku lobzala. Umakhala ndi zokolola zochuluka pa hekitala.

Malimba

Umagwiritsidwa ntchito ngati nsinjiro. Umachita bwino m’madera aku chigwa cha mtsinje wa Shire ndi m’mphepete mwa nyanja. Umakhwima pakati pa matsiku 110 ndi 120 kuchokera tsiku lobzala.

RG1

Umagwiritsidya ntchito ngati nsinjiro. Umalimidwa ku Madera komwe kumafala kwambiri matenda a khate monga ku Phalombe. Umakhwima pakatha masiku 130 mpaka 140 kuchokera tsiku lobzala.

Mani-pintar

Mtedzawu amapangira mafuta ophikira. Umalaimidwa ku Madera a m’mphepete mwa nyanja makamaka m’maboma a Nkhotakota, Salima, Mangochi, chigwa cha mtsinje wa Shire, Bwanje ndi Balaka. Umakhwima pakati pa amsiku okwanira 130 mpaka 140 kuchokera tsiku lobzala.

Mawanga

Mtedzawu amapangira mafuta ophikira . Umalimidwa m’madera momwe mumalimidwa mtedza wa manipinta. Ungabzalidwenso m’malo okwera. Mtedzawu umapezeka ndi mafuta ochulukirapo kuposa manipinta.

Nsinjiro (ICGV-SM 90704)

Amapangira nsinjiro. Umalimidwa madera ambiri okwera. Ndiwopirira kumatenda a khate, mumakolola zokolola zochuluka makilogalamu 2000 pa hekitala imodzi. Umakhwima pakati pa miyezi inayi ndi isanu kuchokera tsiku lobzala.

Kakoma (JL 24)

Amapangira nsinjiro. Umachita bwino Madera otsika adziko lino. Umachitanso bwino ku dimba (ulimi wamthirira). Umakhwima pakati pa miyezi itatu ndi inayi. Mtedza wake umakhala ung’ono ung’ono ndipo zokolola zake zimakwana makilogalamu 1500 pa hekitala imodzi.

Baka (ICG 12991)

Amapangira nsinjiro. Umachita bwino ku Madera onse otsika a dziko lino komanso kumadimba. Umakhwima pakatha miyezi itatu ndi inayi kuchokera tsiku lobzala