Nthomba yobwera moyambirira -
zimagwira mbewu pomwe zangomera kumene. Zimapangitsa masamba ambewu kuyoyoka ndipo zokolola zimachepa. Matendawa ndiowopsa ku madera akumtunda. Masamba amakhala ndimadontho ozungulira ofiilira pamwamba patsamba ndipo kunsi kwa tsambalo kumaoneka khakhi.
Nthomba zobwera mochedwa –
zimagwira mbewu mochedwerako poyerekeza ndi nthomba yoyamba ija. Masamba amayoyoka zomwe zimachepetsa zokolola. Matendawa ndiowopsa ku madera otsika monga mmphepete mwa nyanja ndi kuchigwa cha mtsinje wa shire.
Dzimbiri –
Matendawa amagwira mbewu nthawi imodzi ndi Nthomba zobwera mochedwa. Masamba amaoneka ndi madontho a mtundu wa chikasu. Madonthowa amapangisa mabowo patsambapo zomwe zimapangisa masamba kusintha mtundu ndikukhala ofiira, kenako masamba amawuma. Poperani mankhwala a Daconil pakatha masabata awiri.
Khate la mtedza -
matendawa amayamba ndi kachirombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus. Amagwira kwambiri mbewu zomwe zobzalidwa mochedwa komanso momwe muli mipata kapena mbewu sizinamele bwino. Mbewu zomwe zagwidwa ndimatendawa sizikhala zobiriwira ndipo sizikula. Bzalani mbewu moyambilira komanso yopilira kumatenda.
Matenda owoletsa tsinde-
Ndimatenda a khate omwe amadziwika ndimayina awa; white mold, sclerotium rot, sclerotium blight, sclerotium wilt, root rot or foot rot. Amapezeka kwambiri kumadera otentherapo. Mitengo ya mbewu imawola. Gaulani mozamitsa, Limani mizere yokwera, Bzalani mbewu zopirira kumatendawa komanso tsatirani Kasinthasintha wa mbewu.
Nsabwe (Aphids)-
Nsabwe nditizilombo tomwe timadya masamba komanso timafalitsa matenda a khate. Bzalani mbewu mmizere ndi mmipata yotalikirana moyenera.
Chiswe-
Chiswe chimadya makoko amtedza zomwe zimapangitsa makoko kukhala osalimba ndipo umasweka pa nthawi yokolola komanso chimabowola ndi kulowa mu mtsitsi wa ukulu wa mbeu. Tizilomboti timapezeka kwambiri nthawi yomwe dothi lidakali ndi chinyontho. Gwiritsani ntchito mtundu wa mbewu umodzi kuti zizakhwime mofanana ndi cholinga chakuti mudzakolole mu nthawi imodzi. Mungathe kugwiritsa ntchito mankhwala opha tizilombo kuti chiswe chichepe m’mundamo.
Mphunzi za pansi-
Zimadula mbewu isanakule komanso zimatha kjuononga mbewu zomwe zayika kale. Popelani mankhwala opha tiziromboti.