Mtedza ndi imodzi mwa mbewu zofunikira kwambiri pachitukuko cha ulimi m’dziko lino. Mu mtedza mumapezeka zakudya zomanga ndikukulitsa thupi, zoteteza kumatenda komanso mafuta. Ndikofunika kwambiri kulimbikisa ulimi wa mtedza makamaka mtedza omwe umagwiritsidwa ntchito popanga mafuta ndi cholinga chofuna kuchepetsa kugula mafuta kuchokera mayiko akunja.
Pomaliza pa phunziloli alimi akuyenera kudziwa:
Njira zabwino zoyenera pa ulimu wa mtedza, mmene angachepetsere matenda ndi tizilombo zowononga mtedza komanso upangiri wabwino osamalira mtedza
Mtedza umakula bwino mmadera okwera, mmadera otentherako komanso umafuna mvula yochulukirapo (1000mm kapena kuposerapo) pachaka. Mtedza umakula bwino m’dothi lophatikizana ndi mchenga (losasunga madzi ambiri). Konzani malo olima mwansanga mvula isanayambe kugwa kuti mudzabzale ndi mvula yoyamba. Zotsalira m’munda ziyenera kukwiriridwa bwino m’dothi pamene mukugalawuza.