Module Articles

Mtedza

Mtedza

Kasamalidwe ka zokolola

Musawaze madzi kumtedza pamene mukusenda chifukwa umachita nkhungu. Sankhani mtedza motengera ndi magiredi ake. Mtedza onse omwe wachita nkhungu utayidwe ndipo usapasidwe ku ziweto. Sungani mtedza pa malo owuma komanso opita mphepo kuti usachite nkhungu yomwe imayambitsa chuku.