Module Articles

Ginger

Ginger

Mitundu

Mitundu (Chichewa)

MAU OTSOGOLERA

Ginger ndi imodzi mwa mbewu yomwe imalimidwa m’Malawi ndikukololedwa chaka chomwecho. Ginger akakololedwa kumene imakhala misisi yopiringizidwa ndi yolukanalukana yotchedwa Races ndi nthambi zotchedwa Fingers. Ginger amagwiritsidwa ntchito ngati zokometsera ndiwo, kuphikira mandasi ndi kupangira mowa. Mbewu ya Ginger imamela bwino mmalo okwera 1500 meters ndipo ndiyopirira munyengo yotenda ndi kwachinyezi. Imafuna Mvula yapakati pa1500mm ndi 3000mm pachaka yogwa bwino pa miyezi isanu ndi itatu. Misisi ya Ginger imadzalidwa m’malo osiyanasiyana komanso osachita Lowe.

Chithunzi chosonyeza mmene Ginger amaonekera.

Cholinga chachikulu ndikuthandiza alimi kuti akhale ndi ukadaulo ndi nzeru pakalimidwe ka Ginger.

Pomaliza pa phunziroli alimi akuyenera kudziwa izi:

  • Kukhala ndi nzeru zopititsira patsogolo ulimi wa ginger.
  • Kasamalidwe kabwino ka ginger.
  • Njira zochepetsera kapena zogonjetsera tizilombo ndi matenda omwe amagwira mbewuyi.
  • Mmene angasamalire misisi ya Ginger nthawi yokolola, ya kudya komanso yogulitsa.

NYENGO YOYENERA PA ULIMI WA GINGER

  • Kutentha – Mitstisi ya Ginger imafuna nyengo yotentha, ndiyopilila kunyengo yotentha ndiponso imamela bwino mmalo okwera mamita 1500.
  • Dothi – Ginger amamera bwino mu mitundu yosiyanasiyana ya dothi labwino komanso losachita lowe.
  • Mvula - Ginger zimakula bwino ndi mvula yochuluka yokwana 1500mm mpaka 3000mm pa chaka.

 MITUNDU YA GINGER

  • Palibe mitundu yovomerezeka ya Ginger. Alimi amalimbikitsidwa kubzala misisi ya Ginger yomwe imapezeka mosavuta.