Mbewu ya Ginger imakololela pakatha miyezi isanu ndi iwiri kapena isanu ndi inayi kuchokera patsiku lodzala.
Pokolola tiyenera kusamala kuti mitsitsi isadulidwe ndipo isaonongeke koma muzu onse uzulidwe moyenera ndi mitsitsi yonse.
Mitsitsi iyenera kutsukidwa bwino ndi madzi ndi kuchotsa dothi lonse.