Module Articles

Ginger

Ginger

Kubzala

Ginger amadzalidwa pogwiritsa ntchito misisi yake. Mitsitsi ya Ginger imayenera kubzalidwa pamene mvula yoyambirira yagwa. Mbewuyi ikachedwetsedwa kudzalidwa zokolola zimachepa ndi 1000 kilogiramu pa hekitala

Kuchuluka kwa mbewu

Kuti alimi akolole zochuluka ndi zokwanira ayenera kubzala mitstisi ya Ginger ya mulingo woyenera pa ekala kapena pa hekitala. Mitsitsi yochuluka mulingo wama kilogiramu 1200 ndi 1800 imabzalidwa pa hekitala imodzi.