kupalila
Munda wa Ginger uyenera kukhala wopanda udzu. Iyi ndi njira imodzi yopewera matenda ndi tizilombo.
kuthana ndi tizilombo
1. Shoot borer
Mbozi zimaboola mbewu ya ginger ndipo imanyala ndi kufa. Poperani mankhwala a Carbaryl kapena Dimethoate ndipo tsatirani malangizo onse akagwiritsidwe ntchito ka mankwalawa. Mbozi zimenezi zikhoza kuonongedwanso pogwiritsa ntchito manja.
kuthana ndi matenda
1. Soft rot
Zizindikiro za matenda amenewa ndi monga: Masamba amasanduka a chikasu ndipo amauma, phukira zimagwa ndipo zimasiya kutulutsa mitsitsi, mkati mwa mitsitsi mumakhala mofewa, mwakuda ndi mowola. Matendawa amakonda mmalo a lowe.
Zizindikiro za misisi yogwidwa ndi matendawa
Pothana ndi matendawa, Mbewu ya Ginger iyenera kusamalidwa, kudzala mmalo omwe si alowe komanso kudzala kasinthasintha wambewu ndi zopanda matenda.
2. Rhizome rot( kuola kwa mitsitsi)
Zizindikiro za matenda amenewa ndi monga: Mitstisi imawola, nthambi zimagwa
Mmene ginger wogwidwa ndimatendawa amaonekera
Pothana ndi matendawa, mitsitsi ya mbewuyi iyenera kusamalidwa, misisi inyikidwe mmankhwala monga Captafol. Popalira mbewuyi tiyenera kuonetsetsa kuti tisaononge mizu kapena misisi yake.
3. Bacterial Wilt ( khate la masamba)
Zizindikiro za matenda amenewa ndi monga: Masamba amasanduka a chikasu ndipo amauma, phukira zimagwa ndipo zimasiya kutulutsa mitsitsi.
Mmene ginger ogwidwa ndi matendawa amaonekera.
Pothana ndi matendawa, mbewuyi iyenera kusamalidwa ndi kudzala kasinthasintha wambewu ndi zopanda matenda.
Kuthana ndi mbozi / mphutsi zammitsitsi
Nematode ndi mphutsi zopezeka mnthaka, mmizere yambeu komanso misisi. Mputsi zimenezi zimaononga kakulidwe ka mbewu ndipo zimachepetsa zokolola.
Pothana ndi tizilomboti, mitsitsi ya Ginger ikuyenera kunyikidwa mu madzi otentha 48 degrees celcius mosachepera mphindi makumi awiri. Munda wa Ginger uyenera kupoperedwa ndi mankhwala oyenera ndipo kasinthasintha wambewu uyenera zina kutsatidwa monga chimanga, kabishi ndi zina.
Chithunzichi chikuonetsa mmene amaonekera mitsitsi ya Ginger yogwidwa ndi mphutsizi