Module Articles

Tomato

Tomato

Mitundu

Mitundu (Chichewa)

MAU OTSOGOLERA

Tomato ndi mbewu imodzi imene imalimidwa kwambiri m’dziko lino, Mbewuyi imalimidwa nyengo zonse kupatula munyengo yotentha kwambiri chifukwa kutentha kwambiri kumalepheletsa makulidwe ndi maberekedwe abwino. Mlimi angathe kukolora pakati pa 18,000 ndi 50,000 kilogalamu potengera mtundu wa mbewu yomwe mwabzala pa hekitala.

Cholinga Chachikulu: kupititsa patsogolo  ukadaulo ndi nzeru pa kalimidwe ka Tomato pakati pa alimi ang’ono’ang’ono ndikuchulukitsa zokolola.

Pakutha pa phunziroli mlimi ayenera kudziwa:

  • Kalimidwe kabwino ndi koyenera ka Tomato
  • Mmene angatetezere Tomato ku matenda ndi tizilombo toononga
  • Mmenne angapitsire patsogolo ulimi wa tomato
  • Mmene angasamalire tomato akamukolola mmunda mwake

NYENGO YOYENERA

  • Tomato amachita bwino mmalo ofunda pa mlingo wa 20-25oC masana komanso 15-17oC usiku.
  • Chinyezi chikachuluka chimatha kupangisa kuti Tomato agwidwe ndi matenda komanso asapse moyenera
  • Mpweya wa chinyezi chochuluka komanso kutentha kumapangitsa kuti tomato alephere kubereka bwino ndipo zipatso zimakhala zing’onozing’ono. Tomato amachedwa kuyamba kupsa

MITUNDU YA TOMATO

Mitundu yovomelezeka ndi:

Money Maker, Marglobe, Tengeru 97, Rodade, Heinz, Homestead Marondera komanso Roma VF