Tizolombo ta mu tomato
- Nsabwe – popopelani mankhwala a Dimethoate 20WP pa mulingo wa 34g mu 14 litres ya madzi.
- Mbozi – popopelani mankhwala a Carbaryl 85WP, 35g mu madzi ochuluka 14 litres mu knapsack sprayer kapena mu 1 liter mukagwiritsa ntchito ULV Sprayer
Kangaude Wofiira:
- amakonda kukhala kunsi kwa masamba ndipo amaoneka amadontho madontho otuwa komanso pa zipatso.
- Amaoneka wachikasu ndipo amakonda kukhala mmagulu
- Amachulukana mwansanga ndipo amatha kuononga tomato wambiri mu nthawi yochepa
Kuchepetsa kwake:
- Nazale iyikidwe kutali ndi mbewu zimene zagwidwa ndi matenda kapena tizilombo
- Wokelani mbewu za mphamvu zokhazokaha; Wonetsetsani kuti mbewu zikulandira madzi ndi chonde chokwanira.
- Bzalani mbewu zimene zimapangitsa kuti tizilombo timene timadya kangaude wofiira tizipezeka mmunda monga nandolo.
- Zulani ndikutentha mbewu zimene zagwidwa ndi kangaude akangoyamba kumene kulowa mmunda.
- Onetsetsani kuti mmunda mwanu mukhale mopanda udzu.
- Popalira, kukwezera kapena kuthira feteleza, malizirani mbali imene mwayiwona kuti yagwidwa ndi matenda kapena tizilombo.
Chidziwitso: Kangaude wofiira amakonda malo otentha ndi opanda chinyezi. Kuchepetsa kutalikirana kwa mbewu kungathandize kuchepetsa kangaude wofiira.
Agulugufe Woyera
- Agulugufe woyera amaononga tomato kuyambira kunazale mpaka kumunda
- Masamba a tomato amene wagwidwa ndi kangaude woyera amaoneka mwachikasu
- Pewani kufesa kapena kuokera mbewu munyengo yomwe kuli a gulugufe woyera ambiri
Kuchepetsa kwake:
- Osanetsetani kuti mmunda mulibe tchire musanabzale mbewu.
- Thirani neem yemwe amachepetsa kuchulukana ndi kukula kwa mbozi ndi kuchepetsa kufalikira kwa tizilombo ta Agulugufe oyera.
- Bzalani mbewu zomwe zimachepetsa a gulugufe woyera.
Matenda
Thuku/ Kafaluvi/Getsi
- Matendawa amapangitsa kufota ndi kufa kwa mbewu ngati kwatetha 32oC ndi kupitilira.
- Mbewu imafota ili ndi masamba obiriwila.
- Mukadula thunthu lofotalo mkati mwake mumakhala mokuda ndipo mukafinya mumatuluka zoyera, zachikasu kapena za phulusa.
- Matenda akakula, mkati mumakhala bowo
Kuchepetsa kwake
- Zulani mbewu zomwe zagwidwa ndi matendawa.
- Bzalani mbewu mwakasinthasintha.
Kufota kwa tomato
- Matendawa akagwira tomato mtengo wake umaduka, mkati mwake mumakhala mizere yofiirira
- Kunsi kwa masamba kumaoneka chikasu
- Masamba a mbali imodzi akhoza kukhala okhudzidwa pamene mbali ina ilibe zizindikiro.
- Masamba amatenda amathothoka okha.
- Matendawa amafala kupyolera mu mbewu komanso mu nthaka.
- Matendawa amachuluka mmalo omwe nthaka yake ndi ya mchenga.
Kuchepetsa kwake
- Bzalani mbewu zovomerezeka ndi zopilira kumatendawa.
- Musaike nazale malo amene matendawa akudziwika kuti adakhalapo
- Thilani manyowa kuti muchepetse mchele wa m’nthaka
- Wonetsetsani kuti musathire feteleza wokulitsa mopitirira muyeso
Chiwawu Chobwera moyambilira
- Masamba amapanga madontho madontho wozungulira angati katondo.
Kuchepetsa kwake
- Bzalani mbewu zovomerezeka ndizopanda matenda.
- Ngati mukugwiritsa ntchito mbewu yanu, gwiritsani ntchito madzi otenthera.
- Tsatilani ulimi wa kasinthasintha ndi mbewu zina zimene sizili mu gulu la tomato
- Zikilani tomato ndi kuchotsa sakasi.
- Popelani mankhwala a copper ngati matendawa apezeka.
Chiwawu Chobwera mochedwa
- Masamba amakhala ndi madotho owoneka obiriwira akamayamba kumene
- Madontho amasintha mtundu ngati katondo ndipo masamba amafota ndikuwuma koma sathothoka.
Kuchepetsa kwake
- Bzalani mbewu zopilira kumatenda.
- Chotsani sakasi ndi kuzikira tomato.
- Tsatirani ulimi wa kasinthasintha.
Blossom end rot (Physiological disorder)
- Matendawa amabwera chifukwa chosowa mchele wa calcium komanso kusathirira mowirikiza.
- Amagwira kunsi kwa chipatso cha tomato.
- Chipatso chimayamba kuwola koma powolapo pamakhala powuma.
Kuchepetsa kwake
- Kuthilirani tomato mokwanira.
- Thilani laimu mu nthaka imene ilibe calcium wokwanira.
- Popelani mbewu ndi 0.5% calcium chloride pamene zayamba kuyika chipatso