Kupalira
- Wonetsetsani kuti mmunda wa tomato mulibe tchire pozulira kapena popalira.
Kuthira Feteleza
- Thirani feteleza wa “B” Compound(wokulitsa) pa mulingo wa 100g pa munda wa 1m mulifupi ndi mulitali pa phando masiku awiri kapena atatu musanawokere.
- Thirani feteleza wa CAN (wobeleketsa) pa mtunda wa 1m mulitali ndi mulifupi pogwiritsa ntchito kapu nambala 22 pakatha masabata asanu (5) mutawokera pa mulingo wa 20g.
NOTE-CHIDZIWITSO: Funsani alangizi a m’dera lanu kuti akufotokozereni feteleza woyenera ndi mlingo wake.
Kusadzira
- Sadzirani masamba ammusi ndi nthambi zosafunikira (sakasi)
- Mtengo wa Tomato utsale ndi nthambi zinayi zokha.
- Chotsani sakasi kuti zipatso zikhale zikuluzikulu bwino, kupanga maluwa mwachangu komanso kuchepesa matenda ndi tizilombo.
Kuzikira Tomato
- Zikirani mitengo kuti tomato akhale choyima komanso asagwe akakhala wabala kwambiri.
- Kuzikira kumathandizira kuti tomato abale mbali zonse mofanana
Kuphimbira
- Kuphimbira kumalimbikitsidwa mmadera otentha kwambiri.
- Kuphimbira kumathandiza kuti madzi asamachoke mwachangu kuchoka munthaka
- Phimbirani mbewu zimene mwalima munjira ya mthirira