Module Articles

Tomato

Tomato

Kusankha Malo

  • Nthaka ikhale ndi chinyezi koma chisachuluke kwambiri.
  • Malo akhale achonde koma osachita lowe  
  • Sankhani malo amene mphepo imaomba bwino kuti muchepetse matenda komanso malo amene sakhala ndi tchire la mgona-mgona
  • Limani/gaulani mozama bwino munda wanu ndipo muthire manyowa okwana 5kg mpaka 10kg pa malo otalika mita imodzi mulitali ndi mulifupi. Mabedi akhale okwera ma sentimita 20-25. Gwiritsani ntchito mabedi apansi mu nyengo ya chilimwe. Konzani njira pakati pa bedi lina ndi linzake.