Module Articles
Tomato
Tomato
Kubzala
Kufesa
- Fesani mbewu ya tomato pa nazale mmizere yopingasa yotalikana 15cm mpaka 30cm pa bedi.
- Pewani kufesa mbewu pa nazale powaza chifukwa izi zimapangitsa kuti kuzulira udzu, kuthira feteleza ndi kupewa matenda kukhale kovuta.
- Khwimitsani mbeu yanu pa nazale pakatsala sabata imodzi musanakawokere kumunda
- Khwimitsani mbeu isanayambe maluwa, zipatso kapena mphukhira.
- Wokelani mbewu zanu pakatha masabata anayi kapena asanu.
Kuchuluka kwa Mbewu
- Wokelani mbande motalikirana 90cm mulitali komanso 60cm mulifupi.
- Chotsani nthambi ndi masamba osafunikira kuti zipatso zidzakhale zikuluzikulu
- Mukaokera pamalo otalikirana 90cm mulitali komanso 60cm mulifupi mukhonza kukhala ndi mitengo ya tomato yokwana 18500 pa hekitala kapena 7400 pa ekala.