Kudya zakudya zakasinthasintha zochokera kumagulu onse a zakudya nkofunikira pomwe mayi asanayime, ali woyembekezera komanso nthawi yomwe akuyamwitsa kuti mwana akule bwino komanso kuti ziwalo zake zipangike bwino.
- Mayi woyembekezera akuyenera kudya zakudya zowonjezera. Chakudya chowonjezera choyamba adye pakati pa nthawi ya chakudya cha m’mawa ndi cha masana ndipo chachiwiri adye pakati pa chakudya cha masana ndi chamadzulo kuti aziwonjezera mphamvu ndi michere yofunikira m’thupi lake komanso la mwana yemwe akuyembekezereyo.
- Amayi oyembekezera omwe akuchita nseru azidya milingo yochepa ya chakudya pafupipafupi, kasanu kapena kasanu ndi kamodzi patsiku.
- Amayi oyembekezera adye zakudya zopatsa thanzi zochokera m’magulu onse asanu ndi limodzi azakudya zomwe zimapezeka kudera lawo tsiku ndi tsiku.
- Amayi oyembekezera asamwe mowa kapena kusuta fodya kuti apewe kuchoka kwa pakati komanso kupewa zilema za ana zodza kamba ka mowa ndi fodya.
- Amayi apakati akuyenera kumwa mankhwala owonjezera magazi motsata ndondomeko za a chipatala kupewa kuchepa kwa magazi m’thupi.
- Maanja agwiritse ntchito mchere omwe uli ndi Ayodini pokonza zakudya kuti akhale ndi ayodini wokwanira m’thupi.