Module Articles

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Mwana obadwa kumene kufikira miyezi isanu ndi umodzi

Kuyamwitsa mkaka wokhawokha ndi njira ya chilengedwe komanso yabwino kwambiri  yodyetsera mwana wakhanda chifukwa imathandiza kuti mwana akhale wa thanzi komanso wa moyo wabwino. M’miyezi isanu ndi umodzi yoyambirira mwana akuyenera kumangoyamwitsidwa basi; uku kumatchedwa kuyamwitsa mwakathithi. Kutanthauza kuti mwana akuyenera kupatsidwa bere lokha osati zakudya ndi zakumwa zina, ngakhale madzi. Kuyamwitsa mwakathithi miyezi isanu ndi umodzi yoyambirira kumateteza mwana kumatenda osiyasiyana monga kutsekula m’mimba ndi matenda am’mapapo.

  • Mayi ayamwitse mwana mwakathithi kuyambira akangobadwa mpaka miyezi isanu ndi umodzi (6) (osampatsa mwana zakudya zina, angakhale madzi).
  • Mayi aziyamwitsa mwana nthawi ina iliyonse imene mwanayo wafuna ngakhale asanalire.
  • Mayi ayamwitse msana ndi usiku omwe kuti mwanayo azimwa mokwanira komanso kuti mayiyu azipanga mkaka wokwanira. Mayi aziyamwitsa mwana ngakhale mwanayo akudwala.
  • Pamene akuyamwitsa mwana, mayi sakuyenera kumagwira ntchito zina koma kukhala malo abwino ndikuyamwitsa.