Module Articles

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Kadyedwe koyenera ka anthu Okalamba

Kawirikawiri anthu okalamba sagwila ntchito yambiri chifukwa minofu yawo imakhala yakhwefuka komanso mafupa awo aguga. Izi zimapangitsa kuti azidwaladwala matenda okhudzana ndi mafupa. Kuwonjezera apo, zofuna za matupi a anthu okalamba zimasintha.

Thanzi la anthu okalamba limatha kukhala losalongosoka pa zifukwa monga izi: mavuto a amano, mankhwala omwe iwo okumwa Kamba ka matenda osiyanasiyana, umphawi, kuiwalaiwala, nkhawa komanso kulumala. Pa chifukwa ichi, nkoyenera kuonetsetsa kuti anthu okalamba ali ndi zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse. Anthu osamalira okalamba ayenera:

  • Kupezeka zakudya za michere yambiri yopatsa thanzi monga: mpunga wa brown, nsima ya mgaiwa ndi za mgulu la nyemba.
  • Kupeleka zipatso ndi zakudya za masamba zimene zimathandizila kugaya zakudya kupewa matenda odzimbidwa.
  • Kuthila zonunkhilitsa ndi zometsela mu zakudya
  • Kupewa kupeleka chakudya chootcha kwambiri
  • Kuyesetsa kuti banja lonse lidyere pamodzi andi anthu okalamba.
  • Kulimbikitsa zakudya zotolatola zopatsa thanzi.
  • Kuwathandiza kuthana ndi mavuto a mano