Mwana akakwanitsa miyezi isanu ndi umodzi (6), mkaka wam’mawere okha siwokwanira kuti mwanayo akule ndi thanzi. Choncho, mwana amafunika zakudya zina zowonjezera pa mkaka wam’mawere.
Zitsanzo za zakudya zowonjezera zomwe mwana angadye kuchokera kumagulu onse asanu ndi limodzi a zakudya ndi: Zakudya zokhutitsa monga phala (lachimanga, mpunga, mchewere, mbatata, mapira), nthochi kapena mbatata yopota zomwe zingamupatse mwana wanu mphamvu. Zakudya zagulu la nyemba monga, nyemba, nsawawa, khobwe, nandolo, nzama, soya ndi kabaifa, zomwe zimamanga thupi. Zakudya zagulu la nyama zomwe zimamanga thupi monga nyama yofewa, nsomba, nkhuku, bakha, mbewa, mbalame, ziwala, mphalabungu komanso mazira. Zipatso monga mango, papaya, nthochi, manachesi/mandarena, malalanje, mapeyala komanso madzi amalambe zomwe zimathandiza kuteteza mwana kumatenda. Masamba obiriwira monga m’nkhwani, khwanya, kholowa, bonongwe, denje, chisoso ndi masamba ena akudimba zomwe zimateteza kumatenda. Zamafuta, monga nsinjiro, mafuta a mtedza, mafuta a soya, mafuta ampendadzuwa, mapeyala, mafuta a kokonati ndi zina zotero.
- Zakudya zowonjezera pa mkaka wa m’mawere kwa ana apakati pa miyezi isanu ndi umodzi (6) ndi miyezi isanu ndi inayi (9)
Kuchokera pa miyezi isanu ndi umodzi (6) mpaka miyezi isanu ndi inayi (9) pitirizani kudyetsa mwana wanu zakudya zofewa ndi zopota kosachepera kawiri patsiku.
- Chakudya monga phala chizikhala cholimbirako osati cha madzimadzi. Chakudya chamadzimadzi sichipeleka mphamvu zokwanila kuti mwana akule ndi thanzi labwino
- Onjezerani mlingo wa zakudya za mwana pang’onopang’ono kuti pofika miyezi isanu ndi inayi (9) akhale akumaliza chakudya chodzadza kapu imodzi ya 250 ml kawiri kapena katatu patsiku.
- Mpatseni mwana mulingo wokwanira masupuni akulu awiri a nsomba, nyama (nkhuku, mbuzi, nkhuku, nkhumba, kalulu, ngumbi, ziwala ndi zina) kosachepera kamodzi patsiku.
- Zakudya izi zimapereka mchere wa aironi wokwanira mthupi.
- Sinjani kapena gayani nsomba kapena nyama (onetsetsani kuti mwachotsa minga ndi mafupa ngati kuli koyenerera kutero).
- Kazingani kapena wotchani matemba/utaka/usipa owuma ndikugaya limodzi ndi chimanga ndipo phikani phala lolimba ndi ufa umenewu.
- Phikani nsomba zaziwisi zothira matimati ndipo mnyenyereni mwana kuti adye.
- Sinjani nyama yomwe mukufuna kumpatsa mwana ndikuyiphika.
- Mpatseni mwana chiwindi chonyenya mukaphika nkhuku.
- Mdyetseni mwana zipatso kawiri kapena kangapo patsiku kuti zimuthandize kumpatsa chilakolako cha chakudya kuti akule ndi thanzi.
- Phikani masamba a banja lonse ndi Mafuta ophikira kapena nsinjiro ndipo mdyetseni mwana masambawa.
- Musampatse mwana zakudya ndi zakumwa zosapatsa thanzi komanso zopanda phindu kuthupi monga filizesi, jigisi, kamba, masuwiti, mabisiketi chifukwa ndizodula koma sizithandizira mwana kuti akule mwa thanzi.
- Mazira kapena zipatso ngati nthonchi, malalanje ndi mandalena/manachesi ndi zotchipa koma zopatsa thanzi.
- Dekhani, ndipo mwansangala mulimbikitseni mwana kuti adye mosakakamizdwa.
- Gwiritsani ntchito mbale yapadera podyetsa mwana ndikuwonetsetsa kuti wamaliza chakudya chomwe wapatsidwa.
- Onjezerani chakudya chachilendo pa zakudya zomwe mumampatsa mwana sabata iliyonse.
- Zakudya zowonjezera pa mkaka wam’mawere kwa mwana wa miyezi isanu ndi inayi (9) kufikira chaka (miyezi 12)
Pa nthawi imeneyi, mwana amakhala akukula mwachangu choncho amafunika zakudya zambiri pafupipafupi koma m’milingo yochepa kuti akule moyenera. Choncho mwana akuyenera kuyamba tsiku lake ndichakudya cha mam’mawa. Pitirizani kumpatsa mwana chakudya cha mam’mawa (kadzutsa/mfisulo) ndipo onjezerani kuchuluka kwa chakudya chomwe mukumpatsa mpaka mwanayo adzafike nsinkhu wakudya chakudya chodzadza kapu imodzi (250 ml) nthawi zonse. Mdyetseni mwana kosachepera katatu tsiku lirilonse.
Amayi kapena munthu osamalira mwana:
- Dyetsani mwana phala lolimba lopangidwa kuchokera kumagulu asanu ndi limodzi. Izi zikuyenera kukhala zakudya zowonjezeredwa michere kufakitale monga Likuni Phala, phala la m’gaiwa ndi nsinjiro, ufa wa soya kapena futali. Izi ndizabwino kudya m’mamawa.
- Mpatseni mwana nsima yofewa ndi ndiwo zosiyanasiyana monga nyemba zokanya/zopota, masamba okanya kuti mwana ayambe kuphunzira kudya zakudya zomwe anthu pakhomopo amadya.
- Nyamulani chakudya cha mwana kuphatikizapo totolatola ngati zipatso kapena chikondamoyo chophikidwa ndi ufa wowonjezeredwa zakudya zina mukamachoka pakhomo ndi mwana.
- Sambani m’manja komanso sambitsani mwana m’manja pogwiritsa ntchito sopo ndi madzi otetezedwa, ochita chothilirana, musanadyetse mwana.
- Khalani ndi mwana pomwe akudya chifukwa amadya bwino ngati pali wina womulimbikitsa kuti adye.
- Yambani mwadyetsa mwana mokwanira anthu ena a pabanjapo asanadye.
- Zakudya zowonjezera pa mkaka wa m’mawere mwana akakwanitsa chaka mpaka zaka ziwiri
Kuyambira chaka chimodzi mpaka zaka ziwiri ana amakula mofulumira uku akudutsa m’magawo osiyanasiyana amoyo. Mwachitsanzo, sikelo yawo imawonjezekera katatu pakutha chaka; amayenda ndi kuthamangathamanga (kutanganidwa) zomwe zimawonjezera kufunika kwa michere mthupi. Kuphatikiza apo, mwana amakhala pachiwopsezo chotenga matenda osiyanasiyana pomwe Wayamba kuyendayenda ndikukhudzana ndi zinthu zomwe zamuzungulira. Izinso zimaonjezera kufunika kwa michere yosiyanasiyana mthupi mwake. Ndipofunikanso kupitiriza kuyamwitsa mwana ndikumpatsa zakudya zina zowonjezera
- Amayi pitirizani kuyamwitsa mwana pafupipafupi.
- Muyamwitseni kasanu ndi katatu usana ndi usiku kuti mwana alandire zakudya zokwanira mthupi komanso kuti akhale wathanzi komanso wamphamvu.
- Amayi yambani kuyamwitsa mwana musanamupatse zakudya zina.
- Amayi kapena osamalira mwana:
- Ayenera kudyetsa mwana zakudya zomwe banja lonse limadya koma awonetsetse kuti chakudyacho achinyenyanyenya ndi kuchifewetsa.
- Awonetsetse kuti mwana wadyetsedwa kasanu patsiku, chakudya cha m’mawa, masana ndi madzulo komanso zotolatola mkati mwatsiku (pakati pa chakudya cha mmawa ndi cha masana komanso pakati pa chakudya cha masana ndi chamadzulo).Zakudyazi zitha kukhala zipatso monga izi: malalanje, mango, papaya, nthochi, mavwembe, nanazi, mapeyala ndi zina zotere. Mzakudya izi mumachokera mavitamini ofunikila mthupi. Athanso kumudyetsa ndiwo zamasamba obiriwira zophikidwa m’mafuta monga chisoso, m’nkhwani, moringa, bonongwe, kholowa, tomato, mabiringanya, kaloti, kabichi ndi zina zotere zomwe ziri ndi vitamin A ndi C. Asayiwalenso kupatsa ana zinthu zotolatola monga zikondamoyo, zitumbuwa ndi zina.
- Onjezerani kuchuluka kwa mlingo wa nyama/nsomba/mazira zomwe mumapatsa mwana.
- Onjezerani kuchuluka kwa chakudya chompatsa mwana kuti akamafika zaka ziwiri akhale akudya chakudya chokwanira masupuni akulu khumi, mphambu zisanu ndi imodzi (16) patsiku.
- Ana a Zaka ziwri mpaka zaka Zisanu
Pa nthawi iyi ana aleka kuyamwa koma akadakulabe mowilikiza.
- Amayi kapena osamalira mwana ayenera kudyetsa mwana zakudya zomwe banja lonse limadya koma awonetsetse kuti chakudyacho achinyenyanyenya ndi kuchifewetsa.
- Onetsetsani kuti mwana wadyetsedwa kasanu patsiku, chakudya cha m’mawa, masana ndi madzulo komanso zotolatola mkati mwatsiku (pakati pa chakudya cha mmawa ndi cha masana komanso pakati pa chakudya cha masana ndi chamadzulo).
- Onjezerani kuchuluka kwa mlingo wa nyama/nsomba/mazira zomwe mumapatsa mwana
- Onjezerani kuchuluka kwa chakudya chompatsa mwana kuyekeza ndi msinkhu wake.
Ukhondo ndiofunikira kuti tipewe kutsegula mmimba ndi matenda ena omwe amadza kamba ka umve. Kuti kutsegula mmimba kupewedwe, amayi ndi osamala mwana apange izi:
- Gwilitsani ntchito kapu ndi supuni zotsuka bwino pompatsa mwana
- Sambani m’manja pogwiritsa ntchito sopo ndi madzi otetezedwa, ochita chothilirana, musanakonze chakudya cha mwana kapena musanamudyetse
- Msambitseni mwana m’manja pogwiritsa ntchito sopo ndi madzi otetezedwa, ochita chothilirana, asanayambe kudya.