Module Articles

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Mauthenga a Kadyedwe Koyenera

Mau Otsogolera

Kukhala ndi thanzi la bwino ndi mbali imodzi yofuynikira kuti munthu akhale ndi umoyo wabwino ndi opindula. Kunyetchela ndi vuto lalikulu m’Malawi ndipo anthu a zaka zonse akuyenera kudya zakudya za magulu asanu ndi limodzi (6) zokwanila michere ya protein, kuti akwanitse zofunika mmatupi mwawo. Izi zimathandiza kukula ndi kukhala ndi nzeru zabwino komanso kukhala ndi chitetezo chokwanila m’thupi.   

Anthu onse m’maanja akuyenela kumwa madzi okwanila tsiku lililonse, kugwilitsa ntchito mchere okhala ndi ayodini. Kuti anthu akhale ndi moyo wautali komanso wa thanzi, akuyenera kuchepetsa kadyedwe ka shuga, mchere komanso mafuta. Ndikofunikitsitsa kuti chakudya chonse chikonzedwe mwaukhondo kuti matenda apewedwe. Pali ma gulu ena a anthu amene amafunika kusamalitsa pa chakudya ndi kadyedwe ndipo magulu amenewa afotokozedwa mwa mwandodomeko mmusimu.