Mayi woyamwitsa azidya chakudya china chowonjezera kawiri kuwonjezera pa zakudya zomwe amadya nthawi zonse kuti iye ndi mwana apeze mphamvu ndi michere yokwanira.
Mayi woyamwitsa adye zakudya za kasinthasintha zamagulu asanu ndi limodzi (6) zopezeka m’madera awo tsiku ndi tsiku.
Mayi woyamwitsa asamwe mowa kapena kusuta fodya kuti apewe mavuto ndi matenda a ana amene amadza chifukwa cha mowa ndi fodya.
Mayi woyamwitsa akuyenera kumwa Vitamini A pasanapite masabata asanu ndi atatu (8) atangochira kuti mwana naye alandire Vitamini A kudzera mu mkaka wa mmawere.