11. KUKONZA MASOMPHENYA
Masomphenya ndi zinthu zimene munthu, gulu kapena banja amakhazikitsa kuti adzakhale atakwanitsa pa nthawi imene akhazikitsa. Masomphenya amathandiza kuti munthu, banja kapena gulu athe kukonza ndondomeko ya zimene angapange kuti adzapeze zofuna zawo.
Zofunika polemba Masomphenya
Ndondomeko Yolembera Masomphenya
Masomphenya amawonetsa tsogolo lowala. Timajambula monga tayelekedzera m’musimu.
1. Jambulani zomwe muli nazo pakalipano mu mpira oyamba (circle 1).
2. Jambulani zomwe mukufunitsitsa mutakhalanazo pa zaka zitatu zikubwerazo - masomphenya (circle 2).
3. Fufuzani ndikujambula mwayi kapena zomwe zingakuthandizireni kukwaniritsa masomphenya anu (opportunities to achieve your vision).
4. Fufuzani ndikujambula zokulepheretsani/zokupingani kukwaniritsa masomphenya anu (constraints to achieve your vision).
5. Jambula milozo (zomwe mukufuna kukwaniritsa) chaka ndi chaka kufikira zaka zitatu molingana ndi masomphenya anu m’mipira yolembedwa 5. Kumbukirani kuti 5 oyambilira akuyimilira chaka choyamba.
6. Jambulani zintchito zomwe mudzigwira kapena kuchita kuti mupeze zomwe mwajambula m’mulozo (zomwe mukufuna kukwaniritsa). Izi zilembedwe pa mlozo uliwonse (chaka ndi chaka).
CHITSANZO CHA MASOMPHENYA
KALONDOLONDO WA MASOMPHENYA
Dzina la Banja: Chaka:
Masomphenya: Tsiku lopangila kalondolondo:
Mlozo (Milestone) |
Ntchito (Activities) |
Kalozera (Indicator) |
Zomwe zachitika (Progress in the reporting period) |
Ndemanga (zolepheletsa/makonsedwe ake) Comments (Challenges and recommendations) |
Kugula malata 15 omangila nyumba |
Kulima ndi kugulitsa matumba 50 a soya omwe akolola |
Mlingo wa matumba |
Sitinakolore |
Malo okwanila ma hekita 3 analimidwa |
|
Kulima ndi kugulitsa chimanga kudzera mu ulimi wa nthilira
|
Mlingo wa Chimanga |
Sitinayambe kugulitsa
|
Chimanga chili mmunda ndipo chikumera bwino |
|
Kugula malata
|
Mlingo wa malata |
Tagulapo malata 5
|
Matumba 10 osala agulidwa tikagulisa soya ndi chimanga |